36
Kubwezeretsedwa kwa Israeli
1 “Iwe mwana wa munthu, yankhula kwa mapiri a Israeli ndipo unene kuti, ‘Inu mapiri a Israeli, imvani mawu a Yehova.’
2 Ine Ambuye Yehova ndikuti: Mdani wanu ankanena kuti, ‘Aa! Dziko lamapiri lakalekale lija lasanduka lathu.’
3 Choncho nenera ndipo uwawuze kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Popeza anakusakazani ndi kukuponderezani ku mbali zonse motero kuti munakhala mʼmanja mwa anthu a mitundu ina yonse ndipo anthu ankakunenani ndi kukunyozani,
4 choncho, inu mapiri a Israeli, imvani zimene Ine Ambuye Yehova ndikuwuza mapiri ndi magomo, zigwembe ndi zigwa, mabwinja ndi mizinda yosiyidwa imene yakhala ikufunkhidwa komanso kunyozedwa ndi anthu a mitundu ina okuzungulirani.
5 Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti: Mu mkwiyo wanga woopsa ndinayankhula kuyimba mlandu mitundu ina yonse ya anthu makamaka a ku Edomu. Iwowa mwa chimwemwe chodzaza tsaya ndi mwa nkhwidzi analanda dziko langa ndi kulisandutsa lawo ndi kutengeratu dziko la msipu kukhala lawo.’
6 Nʼchifukwa chake, lengeza ku dziko la Israeli, ndipo uwuze mapiri ndi magomo, zigwembe ndi zigwa kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndikuyankhula ndi mtima wokwiya kwambiri chifukwa inu munalandira chitonzo cha anthu a mitundu ina.’
7 Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndikulumbira nditakweza dzanja langa kuti mitundu ya anthu idzatozedwanso.
8 “Koma Inu mapiri a Israeli mudzaphukanso nthambi ndipo mudzawabalira zipatso anthu anga a Israeli, pakuti ali pafupi kubwerera kwawo.
9 Taonani, Ine ndili mbali yanu ndipo ndidzakukomerani mtima. Mudzalimidwa ndi kudzalidwa.
10 Ndidzachulukitsa chiwerengero cha anthu anu, nyumba yonse ya Israeli. Mʼmizinda mudzakhalanso anthu ndipo mabwinja adzamangidwanso.
11 Ndidzachulukitsa chiwerengero cha amuna pamodzi ndi ziweto zomwe, ndipo adzachuluka kwambiri ndi kubereka ana ambiri. Ndidzakhazika anthu mʼdzikomo monga analili kale, ndi kukulemeretsani kuposa kale. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
12 Ndidzachititsa anthu kuyenda pa inu, ndiye kuti inu anthu anga Aisraeli. Iwowo adzakhazikika pa inu, ndipo inu mudzakhala cholowa chawo. Simudzalandanso ana awo.
13 “Ine Ambuye Yehova ndikuti: Popeza anthu amanena kuti, ndiwe dziko limene limadya anthu ake ‘kulanda ana a mtundu wake,’
14 nʼchifukwa chake, simudzadyanso anthu kapena kulanda ana a mtundu wako. Ine Ambuye Yehova ndikutero.
15 Sindidzakulolaninso kumva mnyozo wa anthu a mitundu ina, kapena kupirira kunyogodola kwawo kapenanso kupunthwitsanso anthu a mʼdziko lako. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”
16 Yehova anandiyankhulanso kuti:
17 “Iwe mwana wa munthu, pamene anthu a Israeli ankakhala mʼdziko lawolawo, analiyipitsa ndi makhalidwe awo ndiponso zochita zawo. Machitidwe awo pamaso panga anali onyansa pa zachipembedzo ngati msambo wa mkazi amene ali pa nthawi yake.
18 Tsono ndinawalanga chifukwa cha magazi amene anakhetsa mʼdzikomo, ndiponso chifukwa anayipitsa dziko ndi mafano awo.
19 Ndinawamwaza pakati pa anthu a mitundu ina ndipo anabalalikira mʼmayiko onse. Ndinawalanga molingana ndi makhalidwe awo ndi zochita zawo.
20 Atafika kwa anthu a mitundu ina, kulikonse kumene anapitako, anayipitsa dzina langa loyera. Zinatero popeza anthu ponena za iwo ankanena kuti, ‘Awa ndi anthu a Yehova, komatu anachotsedwa ku dziko lake.’
21 Koma Ine ndinkadera nkhawa dzina langa loyera, limene Aisraeli analiyipitsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene anapitako.
22 “Nʼchifukwa chake awuze Aisraeliwo kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndidzachita zimene ndidzachitezo osati chifukwa cha inuyo Aisraelinu ayi, koma chifukwa cha dzina langa, limene mwaliyipitsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene munapitako.
23 Ndidzaonetsa chiyero cha dzina langa lotchuka, limene layipitsidwa pakati pawo. Anthu a mitundu inayo atadzazindikira kuti ndaonetsa kudzera mwa inu kuti dzina langa ndi loyera, iwo adzadziwanso kuti Ine ndine Yehova. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
24 “Pakuti Ine ndidzakuchotsani pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzakusonkhanitsani kuchoka ku mayiko onse ndi kukubwezerani ku dziko lanulanu.
25 Ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera mtima. Zonse zimene zimakuyipitsani zidzachoka. Ndidzakuyeretsani pochotsa mafano anu onse.
26 Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kulowetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzachotsa mwa inu mtima wanu wowuma ngati mwala ndi kukupatsani mtima wofewa ngati mnofu.
27 Ndipo ndidzayika Mzimu wanga mwa inu ndipo ndidzakuthandizani kutsatira malangizo anga ndi kukusungitsani mosamala kwambiri malamulo anga.
28 Mudzakhala mʼdziko limene ndinapatsa makolo anu. Mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu.
29 Ndidzakupulumutsani ku zonse zokuyipitsani. Ndidzakuchulukitsirani tirigu ndipo sindidzakugwetseraninso njala.
30 Ndidzachulukitsa zipatso za mʼmitengo yanu ndi zokolola za mʼmunda mwanu, kotero kuti simudzanyozedwanso pakati pa anthu a mitundu ina chifukwa cha njala.
31 Pamenepo mudzakumbukira makhalidwe anu oyipa ndi ntchito zanu zoyipa. Machimo anu ndi ntchito zanu zonyansa zidzakuchititsa nokha manyazi.
32 Tsono dziwani kuti Ine sindidzachita zimenezi chifukwa cha inuyo ayi, ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse. Ndiyetu chitani manyazi ndipo mugwetse nkhope zanu, inu Aisraeli chifukwa cha makhalidwe anu!
33 “Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa tsiku limene ndidzayeretse machimo anu onse, ndidzayikamonso anthu mʼmizinda yanu, ndipo ndidzamanganso nyumba pa mabwinja.
34 Dziko limene linasanduka chipululu lizidzalimidwanso. Mʼmalo moti aliyense wopitamo alione dzikolo ngati chipululu tsopano adzaliona lolimidwa.
35 Iwo adzati, ‘Dziko ili, limene linali chipululu, lasanduka munda wa Edeni. Mizinda imene inali mabwinja osiyidwa ndi owonongedwa, tsopano ndi yotetezedwa ndi yokhalamo anthu.
36 Ndipo anthu a mitundu ina okhala pafupi nanu amene anatsala adzadziwa kuti Ine Yehova ndine amene ndinamanganso mizinda yowonongeka ndi kudzalanso zinthu zatsopano mʼmalo mʼmene munali chipululu. Ine Yehova ndayankhula ndipo ndidzazichitadi.’
37 “Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzalolanso Aisraeli kuti andipemphe zoti ndiwachitire: Ndidzachulukitsa anthu awo ngati nkhosa.
38 Adzachulukadi ngati nkhosa zomwe ankapereka ngati nsembe ku Yerusalemu pa nthawi za chikondwerero. Choncho mizinda ya mabwinja idzadzaza ndi anthu. Zikadzatero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”