35
Za Chilango cha Edomu
1 Yehova anandiyankhula kuti:
2 “Iwe mwana wa munthu, yangʼana phiri la Seiri; yankhula moliyimba mlandu ndipo
3 awawuze anthu a kumeneko kuti zimene ndikuyankhula Ine Ambuye Yehova ndi izi: Inu anthu a ku mapiri a Seiri ndikudana nanu. Ndidzatambasula dzanja langa kulimbana nanu, ndipo ndidzasandutsa dziko lanu kukhala chipululu.
4 Mizinda yanu ndidzayisandutsa mabwinja, ndipo dziko lanu lidzasanduka chipululu. Zikadzachitika izi mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
5 “Munali adani a Israeli nthawi zonse, ndipo munkalola kuti Aisraeli aphedwe pa nkhondo pa nthawi ya mavuto awo, pa nthawi imene chilango chawo chinafika pachimake.
6 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pali Ine wamoyo, ndithu ndidzakukanthani. Imfa idzakulondolani. Popeza sunadane nako kukhetsa magazi, imfa idzakulondola.
7 Phiri la Seiri ndidzalisandutsa chipululu ndipo ndidzapha onse amene amapita nabwerera kumeneko.
8 Ndidzaza mapiri ake ndi mitembo. Ophedwa pa nkhondo adzagwera pa zitunda zanu, zigwa zanu ndi mʼmitsinje yanu yonse.
9 Ndidzasandutsa dziko lanu kukhala chipululu mpaka muyaya, ndipo mʼmizinda yanu simudzakhalanso anthu. Zikadzachitika izi mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
10 “Inu munanena kuti, ‘Mitundu iwiri iyi ya anthu, Yuda ndi Israeli, pamodzi ndi mayiko awo omwe idzakhala yathu.’ Munanena chomwechi ngakhale kuti Ine Yehova ndinali momwemo.
11 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pali Ine wamoyo, ndithu ndidzachita nanu monga munachita ndi anthu a ku Yuda ndi Israeli poonetsa mkwiyo wanu, nsanje yanu ndi chidani chanu pa iwo. Ndikadzakulangani mudzandidziwadi pakati panupo.
12 Ndipo mudzadziwa kuti Ine Yehova ndinamva mawu anu onse onyoza amene munanena molimbana ndi mapiri a Israeli. Inu munati, ‘Mapiri a Israeli asanduka bwinja, ndipo aperekedwa kwa ife kuti tiwawononge.’
13 Mawu anu amene munayankhula monyada kundinyoza Ine ndinawamva.
14 Ine Ambuye Yehova ndikuti: Dziko lonse lapansi lidzasangalala pamene ndidzakusandutsani bwinja.
15 Monga momwe inu munasangalala pamene anthu anga Aisraeli anagwa, Inenso ndidzakuchitani chimodzimodzi. Udzasanduka bwinja, iwe Phiri la Seiri, iwe ndi dziko lonse la Edomu. Zikadzatero anthu onse adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”