3
Tsogolo la Yerusalemu 
 
1 Tsoka kwa mzinda wa anthu opondereza,  
owukira ndi odetsedwa!   
2 Sumvera aliyense,  
sulandira chidzudzulo.  
Sumadalira Yehova,  
suyandikira pafupi ndi Mulungu wake.   
3 Akuluakulu ake ali ngati mikango yobuma,  
olamulira ake ndi olusa ngati mimbulu ya nthawi ya madzulo,  
zimene pofika mmawa sizisiya chilichonse.   
4 Aneneri ake ndi odzikuza;  
anthu achinyengo.  
Ansembe ake amadetsa malo opatulika  
ndipo amaphwanya lamulo.   
5 Yehova amene ali pakati pawo ndi wolungama;  
Iye salakwa.  
Tsiku ndi tsiku amaweruza molungama,  
ndipo tsiku lililonse salephera,  
komabe ochita zoyipa sachita manyazi nʼkomwe.   
6 “Ndachotseratu mitundu ya anthu;  
ndagwetsa malinga awo.  
Ndipo sindinasiye ndi mmodzi yemwe mʼmisewu mwawo,  
popanda aliyense wodutsa.  
Mizinda yawo yawonongedwa;  
palibe aliyense adzatsalemo.   
7 Ndinati,  
‘Ndithudi, anthu a mu mzindawu adzandiopa  
ndi kumvera kudzudzula kwanga!’  
Ndipo sindidzawononga nyumba zawo,  
kapena kuwalanganso.  
Koma iwo anali okonzeka  
kuchita mwachinyengo zinthu zonse zimene amachita.   
8 Choncho mundidikire,” akutero Yehova,  
“chifukwa cha tsiku limene ndidzaperekera umboni.  
Ndatsimikiza kusonkhanitsa pamodzi mitundu ya anthu,  
kusonkhanitsa maufumu  
ndi kutsanulira ukali wanga pa iwo;  
mkwiyo wanga wonse woopsa.  
Dziko lonse lidzatenthedwa  
ndi moto wa mkwiyo wa nsanje yanga.   
   
 
9 “Pamenepo ndidzayeretsa milomo ya anthu a mitundu yonse  
kuti anthu onsewo ayitane dzina la Yehova  
ndi kumutumikira Iye pamodzi.   
10 Kuchokera kutsidya kwa mitsinje ya ku Kusi  
anthu anga ondipembedza, omwazikana,  
adzandibweretsera zopereka.   
11 Tsiku limenelo simudzachita manyazi  
chifukwa cha zoyipa zonse munandichitira,  
popeza ndidzachotsa onse mu mzinda uwu  
amene amakondwera chifukwa cha kunyada kwawo.  
Simudzakhalanso odzikuza  
mʼphiri langa lopatulika.   
12 Koma ndidzasiya pakati panu  
anthu ofatsa ndi odzichepetsa,  
amene amadalira dzina la Yehova.   
13 Aisraeli otsala sadzachitanso zolakwika;  
sadzayankhulanso zonama,  
ngakhale chinyengo sichidzatuluka mʼkamwa mwawo.  
Adzadya ndi kugona  
ndipo palibe amene adzawachititse mantha.”   
   
 
14 Imba, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni;  
fuwula mokweza, iwe Israeli!  
Sangalala ndi kukondwera ndi mtima wako wonse,  
iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu!   
15 Yehova wachotsa chilango chako,  
wabweza mdani wako.  
Yehova, Mfumu ya Israeli, ali pakati pako;  
sudzaopanso chilichonse.   
16 Pa tsiku limenelo adzanena kwa Yerusalemu kuti,  
“Usaope, iwe Ziyoni;  
usafowoke.   
17 Yehova Mulungu wako ali pakati pako,  
ali ndi mphamvu yopulumutsa.  
Adzakondwera kwambiri mwa iwe,  
adzakukhalitsa chete ndi chikondi chake,  
adzayimba mokondwera chifukwa cha iwe.”   
   
 
18 “Ndidzakuchotserani zowawa  
za pa zikondwerero zoyikika;  
nʼzolemetsa ndi zochititsa manyazi.   
19 Taonani, nthawi imeneyo ndidzathana ndi  
onse amene anakuponderezani;  
ndidzapulumutsa olumala  
ndi kusonkhanitsa amene anamwazika.  
Ndidzawayamikira ndi kuwachitira ulemu  
mʼdziko lililonse mmene anachititsidwa manyazi.   
20 Pa nthawi imeneyo ndidzakusonkhanitsani;  
pa nthawi imeneyo ndidzakubweretsani ku mudzi kwanu.  
Ndidzakuyamikirani ndi kukuchitirani ulemu  
pakati pa mitundu ya anthu a dziko lapansi  
pamene ndidzabwezeretsa mtendere wanu  
inu mukuona,”  
akutero Yehova.