Zefaniya   
1
1 Yehova anayankhula ndi Zefaniya mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya pa nthawi ya Yosiya, mwana wa Amoni, mfumu ya Yuda.   
Yehova Adzaweruza Dziko Lapansi 
 
2 “Ndidzawononga kotheratu zinthu zonse  
pa dziko lapansi,”  
akutero Yehova.   
3 “Ndidzawononga anthu pamodzi ndi nyama zomwe;  
ndidzawononga mbalame zamlengalenga  
ndi nsomba za mʼnyanja.  
Ndidzawononga anthu oyipa,  
ndipo ndidzafafaniza mtundu wa anthu pa dziko lonse lapansi,”  
akutero Yehova.   
Chenjezo kwa Yuda 
 
4 Ndidzatambasula dzanja langa pa Yuda  
ndi onse okhala mu Yerusalemu.  
Ndidzawononga pamalo pano otsalira opembedza Baala,  
mayina a anthu osapembedza pamodzi ndi ansembe a mafano:   
5 amene amagwada pa madenga a nyumba zawo  
kupembedza zolengedwa zamumlengalenga,  
amene amagwada ndi kulumbira mʼdzina la Yehova,  
komanso mʼdzina la Moleki,   
6 amene abwerera mʼmbuyo osatsata Yehova,  
osafunafuna kapena kupempha nzeru kwa Yehova.   
7 Khalani chete pamaso pa Ambuye Yehova,  
chifukwa tsiku la Yehova layandikira.  
Yehova wakonzekera kupereka nsembe;  
wapatula iwo amene wawayitana.   
8 Pa tsiku la nsembe ya Yehova  
ndidzalanga akalonga  
ndi ana aamuna a mfumu  
ndi onse amene amavala  
zovala zachilendo.   
9 Pa tsiku limenelo ndidzalanga  
onse amene safuna kuponda pa chiwundo,  
amene amadzaza nyumba ya ambuye awo  
ndi chiwawa ndi chinyengo.   
   
 
10 “Pa tsiku limenelo,” akutero Yehova,  
“Kufuwula kwakukulu kudzamveka pa Chipata cha Nsomba,  
kulira kwa chisoni kuchokera mʼChigawo Chatsopano,  
ndi phokoso la kugumuka kochokera ku mapiri.   
11 Lirani mwachisoni, inu amene mumakhala kumene kuli msika;  
a malonda anu onse adzapululidwa,  
ndiponso onse amene ali ndi siliva adzawonongedwa.   
12 Pa nthawi imeneyo ndidzafufuzafufuza mu Yerusalemu ndi nyale  
ndi kulanga onse amene sakulabadira,  
amene ali ngati vinyo wosakhutchumulidwa,  
amene amaganiza kuti, ‘Yehova sadzachita chilichonse,  
chabwino kaya choyipa.’   
13 Chuma chawo chidzafunkhidwa,  
nyumba zawo zidzagwetsedwa.  
Adzamanga nyumba,  
koma osakhalamo;  
adzadzala minda ya mpesa  
koma sadzamwako vinyo wake.”   
Tsiku Lalikulu la Yehova 
 
14 Tsiku lalikulu la Yehova layandikira,  
layandikira ndipo lifika msanga.  
Tamverani! Kulira kwa pa tsiku la Yehova kudzakhala kowawa,  
ngakhale munthu wolimba mtima adzalira kwambiri.   
15 Tsiku limenelo lidzakhala la ukali,  
tsiku losautsa ndi lomvetsa chisoni,  
tsiku la mavuto ndi la chiwonongeko,  
tsiku la mdima ndi lachisoni,  
tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani.   
16 Tsiku loliza lipenga ndi la mfuwu wankhondo,  
tsiku la kugwa kwa mizinda yotetezedwa  
ndi nsanja za pa ngodya.   
17 Ndidzabweretsa msautso pa anthu  
ndipo adzayenda ngati anthu osaona,  
chifukwa achimwira Yehova,  
magazi awo adzamwazika ngati fumbi  
ndi mnofu wawo ngati ndowe.   
18 Ngakhale siliva wawo kapena golide wawo  
sadzatha kuwapulumutsa  
pa tsiku la ukali wa Yehova.  
Dziko lonse lapansi lidzanyeka  
mʼmoto wa nsanje yake  
chifukwa adzakantha modzidzimutsa  
onse okhala pa dziko lapansi.