6
1 Onse amene ali mu ukapolo ayenera kuona ambuye awo ngati oyenera kuwachitira ulemu, kuti anthu anganyoze dzina la Mulungu ndi chiphunzitso chathu.
2 Amene ambuye awo ndi okhulupirira, asawapeputse chifukwa ambuye ndi abale mʼchikhulupiriro. Mʼmalo mwake akuyenera kuwatumikira bwino chifukwa ambuye wawo ndi okondedwa monga okhulupirira ndiponso ndi odzipereka kusamalira akapolo awo.
Aphunzitsi Onyenga ndi Kukonda Ndalama
Zinthu izi ukuyenera kuziphunzitsa ndi kuwalamula anthu.
3 Ngati wina aphunzitsa zosiyana ndi zimenezi, wosagwirizana ndi malangizo woona a Ambuye athu Yesu Khristu ndi chiphunzitso cholemekeza Mulungu,
4 ameneyo ndi wodzitukumula ndipo sakudziwa chilichonse. Iyeyo ali ndi maganizo oyipa, wokonda kusemphana mawu ndi kutsutsana. Zimenezi zimabweretsa nsanje, mikangano, mʼnyozo, kuganizirana zoyipa,
5 ndi kulimbana kosatha pakati pa anthu amitima yopotoka amene alandidwa choonadi ndipo amaganiza kuti kulemekeza Mulungu ndi njira yopezera chuma.
6 Koma kulemekeza Mulungu kuli ndi phindu lalikulu.
7 Pakuti sitinabweretse kanthu mʼdziko lapansi, ndipo sitingatengenso kanthu pochoka mʼdziko lapansi.
8 Koma ngati tili ndi chakudya ndi zovala, zimenezi zitikwanire.
9 Anthu amene amafuna kulemera amagwa mʼmayesero ndi mu msampha ndi mʼzilakolako zambiri zopusa ndi zoopsa zimene zimagwetsera anthu mʼchitayiko ndi mʼchiwonongeko.
10 Pakuti kukonda ndalama ndiye muzu wa zoyipa za mitundu yonse. Anthu ena ofunitsitsa ndalama, asochera ndipo asiya njira yachikhulupiriro ndipo adzitengera zowawitsa zambiri.
Malangizo Otsiriza kwa Timoteyo
11 Koma iwe, munthu wa Mulungu, thawa zinthu zonsezi. Tsatira chilungamo, moyo wolemekeza Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, kupirira ndi kufatsa.
12 Menya nkhondo yabwino yachikhulupiriro. Gwiritsitsa moyo wosatha umene anakuyitanira pamene unavomereza bwino lomwe pamaso pa mboni zambiri.
13 Ndikukulamula pamaso pa Mulungu amene amapatsa moyo zinthu zonse, ndiponso pamaso pa Khristu Yesu amene pochitira umboni pamaso pa Pontiyo Pilato, ananena zoona zenizeni.
14 Usunge lamuloli mopanda banga ndi cholakwa kufikira Ambuye athu Yesu Khristu ataonekera.
15 Pa nthawi yake Mulungu adzamubweretsa kwa ife. Mulungu ndi wodalitsika ndipo Iye yekha ndiye Wolamulira, Mfumu ya mafumu, Mbuye wa ambuye.
16 Ndiye yekha wosafa ndipo amakhala mʼkuwala koopsa. Mulungu amene munthu aliyense sanamuone. Kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu mpaka muyaya. Ameni.
Za Kudalira Chuma
17 Anthu onse amene ali ndi chuma uwalamule kuti asanyade kapena kuyika mitima yawo pa chuma chimene nʼchosadalirika. Koma chiyembekezo chawo chikhale mwa Mulungu amene amatipatsa mowolowamanja zonse zotisangalatsa.
18 Uwalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, owolowamanja ndi okonda kugawana zinthu zawo ndi anzawo.
19 Potero adzadziwunjikira chuma chokhalitsa ngati maziko okhazikika a nthawi zakutsogolo, kuti akalandire moyo, umene ndi moyo weniweni.
Mawu Otsiriza
20 Timoteyo, samalitsa zimene unapatsidwa. Upewe nkhani zopanda pake zosalemekeza Mulungu ndiponso maganizo otsutsana amene amaganizidwa molakwika kuti ndi nzeru.
21 Anthu ena chifukwa chovomereza nzeru zotere, asochera nʼkutaya chikhulupiriro chawo.
Chisomo chikhale nawe.