5
Mwamuna  
1 Ndalowa mʼmunda mwanga, iwe mlongo wanga, iwe mkwatibwi wanga;  
ndasonkhanitsa mure wanga ndi zokometsera zakudya zanga.  
Ndadya uchi wanga pamodzi ndi zisa zake zomwe;  
ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga.  
Abwenzi  
Idyani abwenzi anga, imwani;  
Inu okondana, imwani kwambiri.   
Mkazi  
2 Ndinagona tulo koma mtima wanga unali maso.  
Tamverani, bwenzi langa akugogoda:  
“Nditsekulire, mlongo wanga, bwenzi langa,  
nkhunda yanga, wangwiro wanga.  
Mutu wanga wanyowa ndi mame,  
tsitsi langa lanyowa chifukwa cha nkhungu ya usiku.”   
3 Ndavula kale zovala zanga,  
kodi ndizivalenso?  
Ndasamba kale mapazi anga  
kodi ndiwadetsenso?   
4 Bwenzi langa anapisa dzanja lake pa chibowo cha pa chitseko;  
mtima wanga unagunda chifukwa cha iye.   
5 Ndinanyamuka kukamutsekulira wachikondi wangayo,  
ndipo manja anga anali noninoni ndi mure,  
zala zanga zinali mure chuchuchu,  
pa zogwirira za chotsekera.   
6 Ndinamutsekulira wachikondi wanga,  
koma nʼkuti wachikondi wangayo atachoka; iye anali atapita.  
Mtima wanga unafumuka chifukwa cha kuchoka kwake.  
Ndinamuyangʼanayangʼana koma sindinamupeze.  
Ndinamuyitana koma sanandiyankhe.   
7 Alonda anandipeza  
pamene ankayendera mzindawo.  
Anandimenya ndipo anandipweteka;  
iwo anandilanda mwinjiro wanga,  
alonda a pa khoma aja!   
8 Inu akazi a ku Yerusalemu ndithu ndikukupemphani,  
mukapeza wokondedwa wangayo,  
kodi mudzamuwuza chiyani?  
Muwuzeni kuti ine ndadwala nacho chikondi.   
Abwenzi  
9 Iwe wokongola kuposa akazi onsewa,  
kodi wokondedwa wakoyo ndi wopambana wina aliyense bwanji?  
Kodi wokondedwa wakoyo ndi wopambana ena onse chotani  
kuti uzichita kutipempha motere?   
Mkazi  
10 Wokondedwa wangayo ndi wowala kwambiri ndi wathanzi  
pakati pa anthu 1,000.   
11 Mutu wake ndi golide woyengeka bwino;  
tsitsi lake ndi lopotanapotana,  
ndiponso lakuda bwino ngati khwangwala.   
12 Maso ake ali ngati nkhunda  
mʼmbali mwa mitsinje ya madzi,  
ngati nkhunda zitasamba mu mkaka,  
zitayima ngati miyala yamtengowapatali.   
13 Masaya ake ali ngati timinda ta mbewu zokometsera zakudya  
zopatsa fungo lokoma.  
Milomo yake ili ngati maluwa okongola  
amene akuchucha mure.   
14 Manja ake ali ngati ndodo zagolide  
zokongoletsedwa ndi miyala yamtengowapatali.  
Thupi lake ndi losalala ngati mnyanga wanjovu  
woyikamo miyala ya safiro.   
15 Miyendo yake ili ngati mizati yamwala,  
yokhazikika pa maziko a golide.  
Maonekedwe ake ali ngati Lebanoni,  
abwino kwambiri ngati mkungudza.   
16 Milomo yake ndi yosangalatsa kwambiri;  
munthuyo ndi wokongola kwambiri!  
Uyu ndiye wachikondi wanga ndi bwenzi langa,  
inu akazi a ku Yerusalemu.