20
Davide ndi Yonatani
1 Tsono Davide anathawa ku Nayoti ku Rama ndi kupita kwa Yonatani ndipo anamufunsa kuti, “Kodi ine ndinachita chiyani? Kodi ndinalakwa chiyani? Kodi abambo ako ndinawalakwira chiyani kuti azifuna kundipha?”
2 Yonatani anayankha kuti, “Sizitheka! Iwe sufa ayi! Taona abambo anga sachita chinthu chilichonse chachikulu kapena chachingʼono wosandiwuza ine. Tsopano abambo anga angandibisire bwanji zimenezi? Sichoncho ayi.”
3 Koma Davide analumbira kuti, “Abambo ako akudziwa bwino lomwe kuti iwe umandikonda ndipo iwo amaganiza kuti, Yonatani sayenera kudziwa zimenezi mwina adzamva chisoni kwambiri. Komabe, pali Yehova ndi pali iwe, imfa sinanditalikire.”
4 Yonatani anawuza Davide kuti, “Chilichonse chimene iwe ukufuna kuti ndichite, ndidzakuchitira.”
5 Ndipo Davide anati, “Taona mawa ndi tsiku la chikondwerero cha mwezi watsopano, ndipo ine ndiyenera kukadya ndi mfumu. Koma undilole ndipite ndikabisale mʼmunda mpaka mkuja madzulo.
6 Ngati abambo ako akafunsa za ine, ukawawuze kuti, ‘Davide anandiwumiriza kuti ndimulole apite msanga kwawo ku Betelehemu, chifukwa akupereka nsembe yapachaka ya banja lonse.’
7 Akanena kuti, ‘Wachita bwino,’ ndiye kuti zinthu zindiyendera bwino ine mtumiki wako. Koma ngati akapsa mtima, ndiye udziwe kuti iwo atsimikiza zondichita zoyipa.
8 Koma undikomere mtima ine mtumiki wako, pakuti unapangana nane pangano pamaso pa Yehova. Ngati ndine wolakwa undiphe ndiwe, koma usandipereke kwa abambo ako.”
9 Yonatani anati, “Sizitheka! Ndikanadziwa kuti abambo anga atsimikiza kuti akuchite choyipa, kodi sindikanakuwuza?”
10 Davide anafunsa kuti, “Adzandiwuza ndani ngati abambo ako akuyankhe mwaukali?”
11 Yonatani anawuza Davide kuti, “Tiyeni tikayende ku mundako.” Ndipo anapita onse awiri.
12 Kenaka Yonatani anawuza Davide kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akhale mboni! Ine ndikadzafunsa abambo anga nthawi yonga ino mmawa kapena mkuja, ndipo ndikadzapeza kuti akukufunira zabwino, ine ndidzatuma mawu kuti udziwe.
13 Koma ngati abambo anga atsimikiza kukuchita choyipa, Yehova andilange ine Yonatani, ndipotu kwambiri ngati sindidzakudziwitsa ndi kukulola kuti upite mu mtendere. Yehova akhale nawe monga anakhalira ndi abambo anga.
14 Ndikakhalabe ndi moyo udzandionetse kukoma mtima monga kwa Yehova nthawi yonse ya moyo wanga, kuti ine ndisaphedwe.
15 Ndipo usadzaleke kuchitira chifundo banja langa. Pamene Yehova adzawatha adani onse a Davide pa dziko lapansi.”
16 “Dzina la ine Yonatani lisadzafafanizidwe nawo pamodzi. Yehova alange adani onse a Davide.”
17 Kenaka Yonatani anamulumbiritsanso Davide kuti asaleke kumukonda, pakuti ankamukonda monga ankadzikondera yekha.
18 Kenaka Yonatani anawuzanso Davide kuti, “Mawa ndi tsiku la chikondwerero cha mwezi watsopano. Zidzadziwika kuti iwe palibe chifukwa mpando wako udzakhala wopanda munthu.
19 Mkuja adzakufunafuna. Tsono udzapite pamalo pamene unabisala poyamba paja ndipo ukadikire pa mulu wa miyala uli apowo.
20 Ine ndidzaponya mivi itatu pambali pake, ngati ndikulasa chinthu.
21 Ndipo ndidzatuma mnyamata ndi kuti, ‘Pita ukatole miviyo!’ Ngati ndidzanena kwa iye kuti, ‘Taona, mivi ili mbali yakuno, kayitole,’ iwe ukatuluke, pakuti ndikulumbira, pali Yehova Wamoyo, ndiye kuti zako zili bwino, palibe choopsa chilichonse.
22 Koma ndikadzati, ‘Taona mivi ili patsogolo pako,’ iwe udzachoke chifukwa Yehova ndiye walola kuti uchokepo.
23 Tsono zimene tapanganazi Yehova ndiye mboni pakati pa iwe ndi ine mpaka muyaya.”
24 Choncho Davide anakabisala mʼmunda ndipo nthawi ya chikondwerero cha mwezi watsopano itakwana mfumu Sauli anadzakhala pansi kuti adye.
25 Iye anakhala pa malo ake a nthawi zonse pafupi ndi khoma moyangʼanana ndi Yonatani, ndipo Abineri anakhala moyandikana ndi Sauli, koma pa malo a Davide panalibe munthu.
26 Sauli sananene chilichonse tsiku limenelo pakuti ankaganiza kuti “Chilipo chimene chachitika ndi Davide. Mwina mwake ngosayenera za chipembedzo.”
27 Koma pa tsiku lachiwiri la chikondwerero cha mwezi watsopano pamalo pa Davide panalibenso munthu. Kenaka Sauli anafunsa Yonatani kuti, “Nʼchifukwa chiyani mwana wa Yese sanabwere kudzadya, dzulo ngakhale lero?”
28 Yonatani anayankha kuti, “Davide anandiwumiriza kuti ndimulole kuti apite ku Betelehemu.
29 Anati, ‘Undilole ndipite, chifukwa banja lathu likupereka nsembe mu mzindamo ndipo mʼbale wanga wandiwumiriza kuti ndikakhale nawo. Ngati wandikomera mtima, chonde ndilole ndipite ndikaone abale anga.’ Nʼchifukwa chake sanabwere kudzadya ndi mfumu.”
30 Sauli anamupsera mtima Yonatani ndipo namuwuza kuti, “Iwe mwana wobadwa mwa mkazi wamakhalidwe oyipa ndi wowukira! Kodi ukuyesa kuti ine sindikudziwa kuti umagwirizana ndi mwana wa Yese, amene akufuna kukuchititsa manyazi iwe ndi amayi ako?
31 Mwana wa Yese akakhala ndi moyo pa dziko lapansi lino, iwe sudzakhala mfumu. Tsopano tumiza munthu akamutenge kubwera naye kwa ine, pakuti Davide ayenera kufa basi!”
32 Yonatani anafunsa abambo ake kuti, “Nʼchifukwa chiyani mufuna kuti Davide aphedwe? Iye walakwa chiyani?”
33 Apo Sauli anamuponyera mkondo wake kuti amuphe. Tsono Yonatani anadziwa kuti abambo ake atsimikiza mtima kuti aphe Davide.
34 Yonatani anachoka pa tebulopo ali wopsa mtima kwambiri. Tsiku lachiwiri la chikondwererocho Yonatani sanadye chakudya. Iye anawawidwa mtima chifukwa abambo ake anatsimikiza zakupha Davide.
35 Tsono mmawa Yonatani anapita ku munda kumene anapangana ndi Davide. Anali ndi mnyamata wake.
36 Tsono anawuza mnyamatayo kuti, “Thamanga ukatole muvi umene nditi ndiponye.” Mnyamatayo akuthamanga Yonatani anaponya muvi patsogolo pa mnyamatayo.
37 Mnyamatayo atafika pamene muvi wa Yonatani unagwera,
38 Yonatani anayitananso mnyamatayo kuti, “Fulumira, pita msanga usayime.” Choncho mnyamatayo anatola muvi uja ndi kubwera nayo kwa mbuye wake.
39 (Mnyamatayo sanadziwe chimene chimachitika koma Yonatani ndi Davide ndiwo ankadziwa).
40 Pambuyo pake Yonatani anapereka zida zake za nkhondo kwa mnyamatayo ndipo anati, “Pita, nyamula ubwerere nazo ku mzinda.”
41 Mnyamatayo anapita. Kenaka Davide anatuluka ku mbali ina ya mulu wa miyala uja, nadzigwetsa pansi ndi kugunditsa nkhope yake pansi katatu. Anapsompsona nayamba kulira onse awiri, koma Davide analira kwambiri.
42 Yonatani anawuza Davide kuti, “Pita mu mtendere pakuti ife awiri tinalumbira mʼdzina la Yehova kuti, ‘Yehova ndiye akhale mboni pakati pa iwe ndi ine ndiponso pakati pa zidzukulu zako ndi zidzukulu zanga kwa nthawi yonse.’ ” Kenaka Davide anachoka, ndipo Yonatani anabwerera ku mzinda kuja.