21
Kumwamba ndi Dziko Lapansi Zatsopano
1 Kenaka ndinaona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano pakuti kumwamba koyamba ndi dziko lapansi loyamba zinapita ndipo kunalibenso nyanja ina iliyonse.
2 Ndinaona mzinda wopatulika, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu, utakonzedwa ngati mkwatibwi wovala zokongola kukonzekera mwamuna wake.
3 Ndipo ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Mpando Waufumu kuti, “Taonani! Malo wokhalapo Mulungu ali pakati pa anthu, ndipo Iye adzakhala ndi anthuwo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulungu mwini adzakhala nawo nakhala Mulungu wawo.
4 ‘Mulungu adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo. Sikudzakhalanso imfa kapena kukhuza maliro kapena kulira kapena ululu popeza zakale zapita.’ ”
5 Amene anakhala pa mpando waufumuyo anati, “Ndikulenga zinthu zonse zikhale zatsopano!” Ndipo anati, “Lemba izi, pakuti mawu awa ndi okhulupirika ndi woona.”
6 Iye anandiwuza kuti, “Kwatha. Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza. Kwa onse akumva ludzu, ndidzawapatsa zakumwa zaulere zochokera ku kasupe wamadzi amoyo.
7 Iye amene adzapambane adzalandira zonsezi, ndipo ndidzakhala Mulungu wake ndi Iye adzakhala mwana wanga.
8 Koma amantha, osakhulupirira, okonda zonyansa, opha anthu, achiwerewere, amatsenga, opembedza mafano ndi abodza, malo awo adzakhala nyanja yamoto ya sulufule wotentha. Iyi ndi imfa yachiwiri.”
Mzinda wa Yerusalemu Watsopano
9 Mmodzi wa angelo asanu ndi awiri aja, anali ndi mbale zisanu ndi ziwiri zodzaza ndi miliri yotsiriza isanu ndi iwiri anandiwuza kuti, “Bwera, ine ndidzakuonetsa mkwatibwi wa Mwana Wankhosa.”
10 Ndipo anandinyamula mwa Mzimu Woyera kupita nane ku phiri lalikulu ndi lalitali nandionetsa mzinda wopatulika, Yerusalemu ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu.
11 Unawala ndi ulemerero wa Mulungu, ndipo kuthwanima kwake kunali ngati mwala wamtengowapatali, ngati jasipa; woyera ngati krustalo.
12 Mzindawo unali ndi mpanda waukulu ndi wautali, unali ndi zipata khumi ndi ziwiri, ndipo panali angelo khumi ndi awiri. Pa chipata chilichonse panayima mngelo. Pa chipata chilichonse panalembedwa dzina la fuko la Israeli.
13 Kummawa kunali zipata zitatu, kumpoto zitatu, kummwera zitatu ndi kumadzulo zitatu.
14 Mpanda wa mzindawu unali ndi maziko khumi ndi awiri ndipo pa mazikopo panali mayina khumi ndi awiri a atumwi a Mwana Wankhosa.
15 Mngelo amene ankayankhula nane uja anali ndi ndodo yagolide yoyezera mzindawo, zipata zake ndi mpanda wake.
16 Mzindawo unamangidwa mofanana kutalika kwake, mulitali ndi mulifupi munali mofanana. Anayeza mzindawo ndi ndodo ija ndipo anapeza kuti mulitali, mulifupi ndi msinkhu wake kutalika kwake kunali makilomita 2,200.
17 Anayesa mpanda uja ndipo kuchindikala kwake kunali kopitirirapo mamita 65 monga mwa muyeso wa anthu umene mngelo anagwiritsa ntchito.
18 Mpandawo unapangidwa ndi yasipa, ndipo mzindawo unali wagolide oyengeka owala ngati galasi.
19 Maziko a mpanda wa mzindawo anali okongoletsedwa ndi miyala yamtengowapatali ya mtundu uliwonse. Maziko oyamba anali yasipa, achiwiri anali safiro, achitatu ndi kalikedo, achinayi ndi simaragido,
20 achisanu ndi sardiyo, achisanu ndi chiwiri ndi krusolito, achisanu ndi chitatu ndi berulo, achisanu ndi chinayi ndi topaziyo, a khumi ndi krusoprazo, a khumi ndi chimodzi ndi huakito, a khumi ndi chiwiri ndi emetusto.
21 Zipata khumi ndi ziwiri zija zinapangidwa ndi ngale, chipata chilichonse chinapangidwa ndi ngale imodzi. Misewu ya mzindawo inali yopangidwa ndi golide oyengeka, owala ngati galasi.
22 Ine sindinaone Nyumba ya Mulungu iliyonse mu mzindawo chifukwa Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse ndi Mwana Wankhosa ndiwo Nyumba yake.
23 Palibe chifukwa choti dzuwa kapena mwezi ziwale popeza mu mzindawo ulemerero wa Mulungu ndiwo umawalamo ndipo nyale yake ndi Mwana Wankhosa uja.
24 Mitundu ya anthu idzayenda mʼkuwala kwake ndipo mafumu a dziko lapansi adzabweretsa ulemerero wawo mu mzindamo.
25 Zipata zake sizidzatsekedwa ngakhale tsiku limodzi lomwe pakuti sikudzakhala usiku kumeneko.
26 Ulemerero ndi ulemu wa mitundu ya anthu adzapita nazo kumeneko.
27 Kanthu kosayeretsedwa sikadzalowamo, kuphatikizanso aliyense wochita zinthu zochititsa manyazi ndi zachinyengo, koma okhawo amene mayina awo alembedwa mʼbuku lamoyo la Mwana Wankhosa.