17
Mkazi Wachiwerewere
1 Mmodzi wa angelo asanu ndi awiri aja amene anali ndi mbale zisanu ndi ziwiri anadza nati kwa ine, “Bwera ndikuonetse chilango cha mkazi wadama wotchuka uja amene akukhala pambali pa madzi ambiri.
2 Mafumu a dziko lapansi amachita naye chigololo ndipo okhala pa dziko lapansi analedzera ndi vinyo wa zigololo zake.”
3 Kenaka mngeloyo anandinyamula mwa Mzimu Woyera kupita nane ku chipululu. Kumeneko ndinaona mkazi atakhala pa chirombo chofiira chokutidwa ndi mayina a chipongwe ndipo chinali ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.
4 Mkaziyo anavala zovala za pepo ndi zofiira nadzikongoletsa ndi golide, miyala yapamwamba ndi ngale. Ananyamula chikho chagolide mʼdzanja lake, chodzaza ndi zinthu zonyansa ndi fungo loyipa la zigololo zake.
5 Pa mphumi pake panalembedwa dzina lodabwitsa:
BABULONI WAMKULU
MAYI WA AKAZI ADAMA
NDI WAZOYIPITSA ZA DZIKO LAPANSI.
6 Ndinaona kuti mkaziyo anali ataledzera ndi magazi a oyera mtima, magazi a amene anachitira umboni Yesu.
Nditamuona mkaziyo ndinadabwa kwambiri.
7 Kenaka mngelo uja anati kwa ine, “Bwanji ukudabwa? Ndikufotokozera chinsinsi cha mkaziyu ndi chinsinsi cha chirombo chimene wakwerapochi chokhala ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.
8 Chirombo chimene wachionachi chinalipo kale koma tsopano kulibe ndipo chidzatuluka ku chidzenje chakuya ndi kupita kukawonongedwa. Anthu okhala pa dziko lapansi amene mayina awo sanalembedwe mʼbuku lamoyo kuyambira pa kulengedwa kwa dziko lapansi adzadabwa pamene adzaona chirombocho, chifukwa chinalipo kale, tsopano kulibe, komabe chidzabwera.
9 “Zimenezi zikufunika kuganizira mwanzeru. Mitu isanu ndi iwiriyo ndi mapiri asanu ndi awiri pomwe mkazi uja amakhalirapo. Yomweyonso ndi mafumu asanu ndi awiri.
10 Mafumu asanu anagwa, imodzi ilipo ndipo ina sinabwere; koma pamene idzafika, idzayenera kukhala kwa kanthawi kochepa.
11 Chirombo chomwe chinalipo kale ndipo tsopano kulibe ndiyo mfumu yachisanu ndi chitatu. Iyo ndi ya mʼgulu la asanu ndi awiriwo ndipo ikupita kukawonongedwa.
12 “Nyanga khumi unaziona zija ndi mafumu khumi amene sanapatsidwe ulamuliro, koma adzapatsidwa ulamuliro pamodzi ndi chirombo kwa ora limodzi.
13 Mafumuwo ali ndi cholinga chimodzi ndipo adzapereka mphamvu ndi ulamuliro wawo kwa chirombocho.
14 Iwo adzachita nkhondo ndi Mwana Wankhosa, koma Mwana Wankhosayo adzawagonjetsa chifukwa Iye ndi Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu, ndipo amene adzakhala ndi Iye ndi oyitanidwa ake, osankhidwa ndi otsatira ake okhulupirika.”
15 Kenaka mngeloyo anati kwa ine, “Madzi amene unawaona pamene mkazi wadamayo anakhalapo ndiwo anthu ochuluka, mitundu ndi ziyankhulo.
16 Nyanga khumi ndi chirombo unazionazo zidzadya mkazi wadamayo. Zidzamufwifwitsa ndi kumusiya wamaliseche; zidzadya nyama yake ndi kumutentha ndi moto.
17 Pakuti Mulungu wayika ichi mʼmitima mwawo kuti akwaniritse cholinga chake povomerezana kupereka mphamvu zawo zolamulira kwa chirombo, kufikira Mawu a Mulungu atakwaniritsidwa.
18 Mkazi unamuonayo ndi mzinda waukulu umene ulamulira mafumu a dziko lapansi.”