14
Mwana Wankhosa ndi Anthu 144,000
1 Kenaka ndinaona patsogolo panga panali Mwana Wankhosa, atayimirira pa Phiri la Ziyoni, ndipo Iye anali pamodzi ndi anthu 144,000 amene pa mphumi pawo panalembedwa dzina la Mwana Wankhosayo ndi la Atate ake.
2 Ndipo ndinamva liwu lochokera kumwamba ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndiponso ngati kugunda kwamphamvu kwa bingu. Liwu limene ndinamvalo linali ngati a anthu akuyimba azeze awo.
3 Anthuwo ankayimba nyimbo yatsopano patsogolo pa mpando waufumu ndi zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu aja. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatha kuphunzira nyimboyo kupatula anthu 144,000 aja amene anawomboledwa pa dziko lapansi.
4 Awa ndiwo amene sanadzidetse koma anadzisunga ndipo sanadziyipitse ndi akazi. Anthu amenewa ndiwo ankatsatira Mwana Wankhosa kulikonse kumene ankapita. Ndiwo amene anagulidwa pakati pa anthu a dziko lapansi kuti akhale oyambirira kuperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwana Wankhosa.
5 Iwo sananenepo bodza ndipo alibe cholakwa.
Angelo Atatu
6 Kenaka ndinaona mngelo wina akuwuluka mu mlengalenga ndipo anali ndi Uthenga Wabwino wamuyaya woti akalalikire kwa anthu okhala pa dziko lapansi, kwa a mtundu uliwonse, a fuko lililonse, a chiyankhulo chilichonse ndi kwa anthu onse.
7 Mngeloyo anayankhula mokweza mawu kuti, “Wopani Mulungu ndi kumutamanda, chifukwa nthawi yoweruza anthu yafika. Mumupembedze Iye amene analenga thambo, dziko lapansi, nyanja ndi akasupe amadzi.”
8 Mngelo wachiwiri anatsatana naye ndipo anati, “Wagwa! Wagwa Babuloni womveka uja, amene anachititsa anthu a mitundu yonse kumwa vinyo wa zilakolako zake zachigololo.”
9 Mngelo wachitatu anatsatana nawo ndi mawu ofuwula anati, “Ngati wina apembedza chirombo chija ndi fano lake ndi kulembedwa chizindikiro pa mphumi kapena pa dzanja,
10 nayenso adzamwa vinyo waukali wa Mulungu, umene wathiridwa popanda kuchepetsa mphamvu zake mʼchikho cha ukali wa Mulungu. Munthuyo adzazunzidwa ndi moto wamiyala yasulufure pamaso pa angelo oyera ndi pa Mwana Wankhosa.
11 Ndipo utsi wa moto wowazunzawo udzakwera kumwamba mpaka muyaya. Sikudzakhala kupumula usana ndi usiku kwa amene anapembedza chirombo chija ndi fano lake kapena kwa aliyense amene analembedwa chizindikiro cha dzina lake lija.”
12 Pamenepa ndi pofunika kupirira kwa anthu oyera mtima amene amasunga malamulo a Mulungu ndi kukhalabe okhulupirika kwa Yesu.
13 Kenaka ndinamva mawu kuchokera kumwamba akuti, “Lemba kuti, Odala anthu amene akufa ali mwa Ambuye kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo.”
“Inde,” akutero Mzimu, “akapumule ntchito zawo zotopetsa pakuti ntchito zawo zidzawatsata.”
Zokolola za Dziko la Pansi
14 Ndinayangʼana patsogolo panga ndinaona mtambo woyera patakhalapo wina ngati Mwana wa Munthu, kumutu atavala chipewa chaufumu chagolide ndipo mʼdzanja mwake munali chikwakwa chakunthwa.
15 Tsono mngelo wina anatuluka mʼNyumba ya Mulungu nafuwula mwamphamvu kwa uja wokhala pa mtamboyu. Mngeloyo anati, “Tenga chikwakwa chako ndipo kolola, pakuti nthawi yokolola ya dziko la pansi yakwana”
16 Choncho wokhala pa mtambo uja anayamba kukolola dzinthu pa dziko lapansi ndi chikwakwa chakecho.
17 Mngelo wina anatuluka mʼNyumba ya Mulungu kumwamba ndipo nayenso anali ndi chikwakwa chakunthwa.
18 Kenaka mngelo winanso amene amalamulira moto, anatuluka kuchokera ku guwa lansembe nayitana mwamphamvu mngelo uja amene anali ndi chikwakwa chakunthwa chija, nati, “Tenga chikwakwa chako chakunthwacho yamba kudula mphesa za mʼmunda wamphesa wa pa dziko lapansi, pakuti mphesa zapsa kale.”
19 Pamenepo mngeloyo anayambadi kugwiritsa ntchito chikwakwa chake nadula mphesa za dziko lapansi, naziponya mʼchopondera mphesa chachikulu cha ukali woopsa wa Mulungu.
20 Mphesazo zinapondedwa mʼchopondera mphesa kunja kwa mzinda. Mʼchopondera mphesamo munatuluka magazi amene anayenderera ngati mtsinje, kuzama kwake mita ndi theka ndipo kutalika kwake makilomita 300.