26
Uziya Mfumu ya Yuda
1 Kenaka anthu onse a ku Yuda anatenga Uziya amene anali wa zaka 16, namuyika kukhala mfumu mʼmalo mwa Amaziya abambo ake.
2 Iye anamanganso mzinda wa Eloti ndi kuwubwezeranso ku Yuda abambo ake atamwalira.
3 Uziya anali wa zaka 16 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 70. Dzina la amayi ake linali Yekoliya wa ku Yerusalemu.
4 Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Amaziya abambo ake.
5 Iye anapembedza Mulungu nthawi ya Zekariya, amene ankamulangiza za kuopa Mulungu amene anamupatsa chipambano.
6 Iyeyo anapita kukachita nkhondo ndi Afilisti ndipo anagwetsa makoma a Gati, Yabine ndi Asidodi. Ndipo kenaka anamanganso mizinda ya pafupi ndi Asidodi ndi malo ena pafupi ndi Afilisti.
7 Mulungu anamuthandiza polimbana ndi Afilisti ndi Aarabu amene amakhala ku Guri-Baala ndiponso polimbana ndi Ameuni.
8 Aamoni ankabweretsa msonkho kwa Uziya ndipo mbiri yake inamveka mpaka ku malire a dziko la Igupto chifukwa anali wamphamvu kwambiri.
9 Uziya anamanga nsanja ku Yerusalemu ku Chipata Chapangodya, ku Chigwa cha Chipata ndi pokhotera mpanda, ndipo anayikamo chitetezo.
10 Iye anamanganso nsanja ku chipululu ndi kukumbanso zitsime zambiri chifukwa anali ndi ziweto zambiri mʼmbali mwa phiri ndi ku zigwa. Iye anali ndi anthu amene ankagwira ntchito mʼminda yake ndiponso mʼminda yake ya mphesa mʼphiri ndi malo achonde, pakuti ankakonda nthaka.
11 Uziya anali ndi gulu lankhondo lophunzitsidwa bwino, lokonzekera kupita ku nkhondo mʼmagulu monga mwa chiwerengero chawo chimene mlembi Yeiyeli ndi Maaseya anasonkhanitsa motsogozedwa ndi Hananiya mmodzi mwa akuluakulu a mfumu.
12 Chiwerengero chonse cha atsogoleri a mʼmabanja oyangʼanira anthu ochita nkhondo chinali 2,600.
13 Pansi pa ulamuliro wawo panali asilikali 307,500 ophunzitsidwa nkhondo, gulu lamphamvu lothandiza mfumu kulimbana ndi adani ake.
14 Uziya anawapangira asilikaliwo zishango, mikondo, zipewa zankhondo, malaya ankhondo achitsulo, mauta ndi miyala yogendera.
15 Mu Yerusalemu anapanga makina okonzedwa ndi anthu aluso amene amagwiritsidwa ntchito pa malo otetezera a pa nsanja ndi pa ngodya kuponyera mivi ndi kugubuduzira miyala. Mbiri yake inamveka kutali ndi ponseponse pakuti anathandizidwa kwambiri mpaka anakhala wamphamvu kwambiri.
16 Koma pamene Uziya anakhala wamphamvu kwambiri, kunyada kwake kunamuwononga. Iye sanakhulupirike kwa Yehova Mulungu wake, ndipo analowa mʼNyumba ya Yehova kukafukiza lubani pa guwa lofukizira.
17 Wansembe Azariya pamodzi ndi ansembe a Yehova ena 80 olimba mtima anamutsatira.
18 Iwo anatsutsana naye ndipo anati, “Sibwino kuti inu mfumu muzifukiza lubani koma zidzukulu za Aaroni, zimene zinapatulidwa kuti zizifukiza lubani. Chokani pa malo opatulika ano, pakuti inu mwakhala osakhulupirika, ndipo simudzalemekezedwa ndi Yehova Mulungu.”
19 Uziya, amene anali ndi chofukizira mʼmanja mwake wokonzeka kuti afukize lubani, anapsa mtima. Iye anakwiyira ansembewo. Ndipo ansembe aja akuona patsogolo pa guwa lofukizira lubani mʼNyumba ya Mulungu, khate linayamba pamphumi pake.
20 Azariya, mkulu wa ansembe pamodzi ndi ansembe ena onse atamuyangʼana anaona kuti anali ndi khate pamphumi pake, ndipo anamutulutsa mofulumira. Ndipo iye mwini anafulumira kutuluka, chifukwa Yehova anamulanga.
21 Mfumu Uziya anali ndi khate mpaka tsiku limene anamwalira. Iye amakhala mʼnyumba ya yekha ngati wakhate, ndipo samalowa mʼNyumba ya Yehova. Yotamu mwana wake ndiye amayangʼanira nyumba yaufumu ndipo ankalamulira anthu a mʼdzikomo.
22 Ntchito zina za mfumu Uziya, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zinalembedwa ndi mneneri Yesaya mwana wa Amozi.
23 Uziya analondola makolo ake, ndipo anamuyika pamodzi ndi makolo ake ku malo a manda a mafumu, koma osati mʼmanda mwawomo poti anthu anati, “Iyeyu anali ndi khate.” Ndipo Yotamu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.