3
Ana a Davide
1 Ana aamuna a Davide amene anabadwira ku Hebroni anali awa:
Woyamba anali Amnoni, amayi ake anali Ahinoamu wa ku Yezireeli;
wachiwiri anali Danieli, amayi ake anali Abigayeli wa ku Karimeli;
2 wachitatu anali Abisalomu, mwana wa Maaka mwana wa Talimai mfumu ya Gesuri;
wachinayi anali Adoniya amayi ake anali Hagiti;
3 wachisanu anali Sefatiya, amayi ake anali Abitali;
wachisanu ndi chimodzi anali Itireamu, amayi ake anali Egila.
4 Ana asanu ndi mmodzi awa a Davide anabadwira ku Hebroni kumene analamulirako zaka zisanu ndi ziwiri ndi miyezi isanu ndi umodzi.
Davide analamuliranso mu Yerusalemu kwa zaka 33,
5 ndipo ana amene anabadwira ku Yerusalemuko anali awa:
Samua, Sobabu, Natani ndi Solomoni. Ana anayi awa anali a Batisuwa mwana wa Amieli.
6 Anaberekanso Ibihari, Elisua, Elipeleti,
7 Noga, Nefegi, Yafiya,
8 Elisama, Eliada ndi Elifeleti, onse analipo asanu ndi anayi.
9 Onsewa anali ana a Davide, osawerengera ana a azikazi. Ndipo mlongo wawo anali Tamara.
Mafumu a Yuda
10 Mwana wa Solomoni anali Rehabiamu,
Rehabiamu anabereka Abiya,
Abiya anabereka Asa,
Asa anabereka Yehosafati,
11 Yehosafati anabereka Yehoramu,
Yehoramu anabereka Ahaziya,
Ahaziya anabereka Yowasi,
12 Yowasi anabereka Amaziya,
Amaziya anabereka Azariya,
Azariya anabereka Yotamu,
13 Yotamu anabereka Ahazi,
Ahazi anabereka Hezekiya,
Hezekiya anabereka Manase,
14 Manase anabereka Amoni,
Amoni anabereka Yosiya.
15 Ana a Yosiya anali awa:
Yohanani mwana wake woyamba,
Yehoyakimu mwana wake wachiwiri,
Zedekiya mwana wake wachitatu,
Salumu mwana wake wachinayi.
16 Ana a Yehoyakimu:
Yekoniya
ndi Zedekiya mwana wake.
Mayina a Mafumu Utatha Ukapolo
17 Zidzukulu za Yekoniya wa mʼndende zinali izi:
mwana wake Silatieli,
18 Malikiramu, Pedaya, Senazara, Yekamiya, Hosama ndi Nedabiya.
19 Ana a Pedaya anali awa:
Zerubabeli ndi Simei.
Ana a Zerubabeli anali awa:
Mesulamu ndi Hananiya.
Mlongo wawo anali Selomiti.
20 Panalinso ana ena asanu awa:
Hasubu, Oheli, Berekiya, Hasabiya ndi Yusabu-Hesedi.
21 Zidzukulu za Hananiya zinali izi:
Pelatiya ndi Yesaiya, ndiponso ana a Refaya, ana a Arinani, ana a Obadiya ndi ana a Sekaniya.
22 Zidzukulu za Sekaniya zinali izi:
Semaya ndi ana ake:
Hatusi, Igala, Bariya, Neariya ndi Safati. Onse anali asanu ndi mmodzi.
23 Ana a Neariya anali awa:
Eliyoenai, Hezekiya ndi Azirikamu. Onse anali atatu.
24 Ana a Eliyoenai: Hodaviya, Eliyasibu, Pelaya, Akubu,
Yohanani, Delaya ndi Anani, onse anali asanu ndi awiri.