25
Anthu Oyimba Nyimbo 
 
1 Davide ndi atsogoleri a asilikali anapatula ena mwa ana a Asafu, Hemani ndi Yedutuni ku utumiki wa uneneri pogwiritsa ntchito apangwe, azeze ndi ziwaya zamalipenga. Tsopano nawu mndandanda wa anthu amene ankagwira ntchito imeneyi:   
   
 
2 Kuchokera kwa ana a Asafu:  
Zakuri, Yosefe, Netaniya ndi Asareli. Ana a Asafu amalamulidwa ndi Asafu ndipo amanenera moyangʼaniridwa ndi mfumu.   
3 Kwa Yedutuni, kuchokera kwa ana ake:  
Gedaliya, Zeri, Yesaya, Simei, Hasabiya ndi Matitiya. Onse analipo 9 ndipo amayangʼaniridwa ndi Yedutuni abambo awo, amene amanenera pogwiritsa ntchito apangwe poyamika ndi kutamanda Yehova.   
4 Kwa Hemani, kuchokera kwa ana ake:  
Bukiya, Mataniya, Uzieli, Subaeli ndi Yerimoti; Hananiya, Hanani, Eliata, Gidaliti ndi Romamiti-Ezeri; Yosibakasa, Maloti, Hotiri ndi Mahazioti.  
5 Onsewa anali ana a Hemani mlosi wa mfumu. Iye anapatsidwa anawa potsata mawu a Mulungu akuti adzamukweza. Mulungu anapatsa Hemani ana aamuna 14 ndi ana aakazi atatu.   
   
 
6 Anthu onsewa ankayangʼaniridwa ndi makolo awo pa mayimbidwe a mʼNyumba ya Yehova. Iwowatu ankayimba ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe potumikira mʼNyumba ya Mulungu. Koma Asafu, Yedutuni ndi Hemani amayangʼaniridwa ndi mfumu.  
7 Iwo pamodzi ndi abale awo onse ophunzitsidwa ndi aluso loyimbira Yehova chiwerengero chawo chinali 288.  
8 Angʼonoangʼono ndi akulu omwe, mphunzitsi ndi wophunzira yemwe anachita maere pa ntchito zawo.   
   
 
|  
9 Maere woyamba amene anali a Asafu, anagwera Yosefe,  |  | 
|    ana ndi abale ake.  | 12  | 
| Maere achiwiri anagwera Gedaliya,  |  | 
|    ndi abale ake ndi ana ake.  | 12  | 
|   
10 Maere achitatu anagwera Zakuri,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake.  | 12  | 
|   
11 Maere achinayi anagwera Iziri,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake.  | 12  | 
|   
12 Maere achisanu anagwera Netaniya,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake.  | 12  | 
|   
13 Maere achisanu ndi chimodzi anagwera Bukiya,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake.  | 12  | 
|   
14 Maere achisanu ndi chiwiri anagwera Yesarela,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake.  | 12  | 
|   
15 Maere achisanu ndi chitatu anagwera Yeshaya,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake.  | 12  | 
|   
16 Maere achisanu ndi chinayi anagwera Mataniya,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake.  | 12  | 
|   
17 Maere a khumi anagwera Simei,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake.  | 12  | 
|   
18 Maere a 11 anagwera Azareli,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake.  | 12  | 
|   
19 Maere a 12 anagwera Hasabiya,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake.  | 12  | 
|   
20 Maere a 13 anagwera Subaeli,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake.  | 12  | 
|   
21 Maere a 14 anagwera Matitiya,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake.  | 12  | 
|   
22 Maere a 15 anagwera Yeremoti,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake.  | 12  | 
|   
23 Maere a 16 anagwera Hananiya,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake.  | 12  | 
|   
24 Maere a 17 anagwera Yosibakasa,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake.  | 12  | 
|   
25 Maere a 18 anagwera Hanani,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake.  | 12  | 
|   
26 Maere a 19 anagwera Maloti,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake.  | 12  | 
|   
27 Maere a 20 anagwera Eliyata,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake.  | 12  | 
|   
28 Maere a 21 anagwera Hotiri,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake.  | 12  | 
|   
29 Maere a 22 anagwera Gidaliti,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake.  | 12  | 
|   
30 Maere a 23 anagwera Mahazioti,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake.  | 12  | 
|   
31 Maere a 24 anagwera Romamiti-Ezeri,  |  | 
|    ana ake ndi abale ake  | 12.   |