Salimo 87
Salimo la Ana a Kora. 
 
1 Iye wakhazikitsa maziko ake pa phiri loyera;   
2 Yehova amakonda zipata za Ziyoni  
kupambana malo onse okhalamo a Yakobo.   
3 Za ulemerero wako zimakambidwa,  
Iwe mzinda wa Mulungu:  
Sela   
4 “Ndidzanena za Rahabe ndi Babuloni  
pakati pa iwo amene amandidziwa.  
Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi,  
ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’ ”   
   
 
5 Ndithudi, za Ziyoni adzanena kuti,  
“Uyu ndi uyo anabadwira mwa iye,  
ndipo Wammwambamwamba adzakhazikitsa iyeyo.”   
6 Yehova adzalemba mʼbuku la kawundula wa anthu a mitundu ina:  
“Uyu anabadwira mʼZiyoni.”  
Sela   
7 Oyimba ndi ovina omwe adzati,  
“Akasupe anga onse ali mwa iwe.”