Salimo 84
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Gititi. Salimo la ana a Kora. 
 
1 Malo anu okhalamo ndi okomadi,  
Inu Yehova Wamphamvuzonse!   
2 Moyo wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka,  
kufuna mabwalo a Yehova;  
Mtima wanga ndi thupi langa zikufuwulira  
Mulungu wamoyo.   
   
 
3 Ngakhale timba wapeza nyumba yokhalamo,  
ndiponso namzeze wadzipezera yekha chisa,  
kumene amagonekako ana ake  
pafupi ndi guwa lanu la nsembe,  
Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga.   
4 Odala amene amakhala mʼNyumba yanu;  
nthawi zonse amakutamandani.  
Sela
   
   
 
5 Odala amene mphamvu yawo ili mwa Inu,  
mitima yawo ikufunitsitsa kuyenda mʼmisewu yopita ku Ziyoni.   
6 Pamene akudutsa chigwa cha Baka,  
amachisandutsa malo a akasupe;  
mvula ya chizimalupsa imadzazanso mayiwe ake.   
7 Iwo amanka nakulirakulira mphamvu  
mpaka aliyense ataonekera pamaso pa Mulungu mu Ziyoni.   
   
 
8 Imvani pemphero langa, Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse;  
mvereni Inu Mulungu wa Yakobo.  
Sela
   
9 Yangʼanani chishango chathu, Inu Mulungu;  
yangʼanani mokoma mtima pa wodzozedwa wanu.   
   
 
10 Nʼkwabwino kukhala mʼmabwalo anu tsiku limodzi  
kuposa kukhala kwina kwake kwa zaka 1,000;  
Ine ndingakonde kukhala mlonda wa pa khomo la Nyumba ya Mulungu wanga  
kuposa kukhala mʼmatenti a anthu oyipa.   
11 Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa ndi chishango;  
Yehova amapereka chisomo ndi ulemu;  
Iye sawamana zinthu zabwino  
iwo amene amayenda mwangwiro.   
   
 
12 Inu Yehova Wamphamvuzonse,  
wodala ndi munthu amene amakhulupirira Inu.