Salimo 82
Salimo la Asafu. 
 
1 Mulungu akutsogolera msonkhano waukulu;  
Iye akuweruza pakati pa “milungu.”   
   
 
2 “Mudzateteza osalungama mpaka liti,  
ndi kukondera anthu oyipa?   
3 Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye;  
mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika.   
4 Landitsani anthu ofowoka ndi osowa;  
apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa.   
   
 
5 “Iwo sadziwa kanthu, sazindikira kalikonse.  
Amayendayenda mu mdima;  
maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.   
   
 
6 “Ndinati, ‘Inu ndinu Mulungu,  
nonsenu ndinu ana a Wammwambamwamba.’   
7 Koma mudzafa ngati anthu wamba;  
mudzagwa ngati wolamula wina aliyense.”   
   
 
8 Dzukani Inu Mulungu, weruzani dziko lapansi,  
pakuti mayiko onse ndi cholowa chanu.