Salimo 8
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa gititi. Salimo la Davide. 
 
1 Inu Yehova Ambuye athu,  
dzina lanu ndi la lamphamvudi pa dziko lonse lapansi!  
   
 
Inu mwakhazikitsa ulemerero wanu  
mʼmayiko onse akumwamba.   
2 Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda,  
Inu mwakhazikitsa mphamvu  
chifukwa cha adani anu,  
kukhazikitsa bata adani ndi anthu obwezera zoyipa.   
   
 
3 Pamene ndilingalira za mayiko anu akumwamba,  
ntchito ya zala zanu,  
mwezi ndi nyenyezi,  
zimene mwaziyika pa malo ake,   
4 munthu ndani kuti Inu mumamukumbukira,  
ndi mwana wa munthu kuti inu mumacheza naye?   
5 Inu munamupanga kukhala wocheperapo kusiyana ndi zolengedwa zakumwamba  
ndipo mwamuveka ulemerero ndi ulemu.   
   
 
6 Inu munamuyika wolamulira ntchito ya manja anu;  
munayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake;   
7 nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe pamodzi  
ndi nyama zakuthengo,   
8 mbalame zamlengalenga  
ndi nsomba zamʼnyanja  
zonse zimene zimayenda pansi pa nyanja.   
   
 
9 Inu Yehova, Ambuye athu,  
dzina lanu ndi lamphamvudi pa dziko lonse lapansi!