Salimo 79
Salimo la Asafu. 
 
1 Inu Mulungu, anthu a mitundu ina alowerera mʼcholowa chanu;  
ayipitsa Nyumba yanu yoyera,  
asandutsa Yerusalemu kukhala bwinja.   
2 Iwo anapereka mitembo ya atumiki anu  
kwa mbalame zamlengalenga ngati chakudya,  
matupi a oyera mtima anu kwa zirombo za dziko lapansi.   
3 Akhetsa magazi monga madzi  
kuzungulira Yerusalemu yense,  
ndipo palibe wina woti ayike mʼmanda anthu akufa.   
4 Ife ndife chinthu chonyozeka kwa anansi athu,  
choseketsa ndi cholalatiridwa kwa iwo amene atizungulira.   
   
 
5 Mpaka liti Inu Yehova? Kodi mudzakwiya mpaka muyaya?  
Kodi mpaka liti nsanje yanu idzayaka ngati moto?   
6 Khuthulirani ukali wanu pa anthu a mitundu ina  
amene sakudziwani Inu,  
pa maufumu  
amene sayitana pa dzina lanu;   
7 pakuti iwo ameza Yakobo  
ndi kuwononga dziko lawo.   
8 Musatilange chifukwa cha machimo a makolo athu  
chifundo chanu chibwere msanga kukumana nafe,  
pakuti tili ndi chosowa chachikulu.   
   
 
9 Tithandizeni Inu Mulungu Mpulumutsi wathu,  
chifukwa cha ulemerero wa dzina lanu;  
tipulumutseni ndi kutikhululukira machimo athu  
chifukwa cha dzina lanu.   
10 Chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akuti,  
“Ali kuti Mulungu wawo?”  
Ife tikuona, zidziwike pakati pa anthu a mitundu ina  
kuti mumabwezera chilango chifukwa cha magazi amene anakhetsedwa a atumiki anu.   
11 Kubuwula kwa anthu a mʼndende kufike pamaso panu;  
ndi mphamvu ya dzanja lanu  
muwasunge amene aweruzidwa kuti aphedwe.   
   
 
12 Mubwezere kwa anansi athu kasanu nʼkawiri  
kunyoza kumene ananyoza Inu Ambuye.   
13 Pamenepo ife anthu anu, nkhosa za pabusa panu,  
tidzakutamandani kwamuyaya,  
kuchokera mʼbado ndi mʼbado  
tidzafotokoza za matamando anu.