Salimo 75
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Salimo la Asafu. Nyimbo. 
 
1 Tikuthokoza Inu Mulungu,  
tikuthokoza, pakuti dzina lanu lili pafupi nafe,  
anthutu amafotokoza za ntchito zanu zodabwitsa.   
   
 
2 Mumati, “Ine ndimayika nthawi yoyenera,  
ndine amene ndimaweruza mwachilungamo.   
3 Pamene dziko lapansi ndi anthu ake onse anjenjemera,  
ndine amene ndimagwiriziza mizati yake molimba.  
Sela
   
4 Kwa odzitama ndikuti, ‘Musadzitamenso,’  
ndipo kwa oyipa, ‘Musatukulenso nyanga zanu.   
5 Musatukule nyanga zanu motsutsana ndi kumwamba;  
musayankhule ndi khosi losololoka.’ ”   
   
 
6 Kugamula milandu sikuchokera kummawa kapena kumadzulo  
kapena ku chipululu.   
7 Koma ndi Mulungu amene amaweruza:  
Iyeyo amatsitsa wina, nakwezanso wina.   
8 Mʼdzanja la Yehova muli chikho  
chodzaza ndi vinyo wochita thovu, wosakanizidwa ndi zokometsera;  
Iye amamutsanulira pansi ndipo onse oyipa a dziko lapansi  
amamwa ndi senga zake zonse.   
   
 
9 Kunena za ine, ndidzalengeza izi kwamuyaya;  
ndidzayimba matamando kwa Mulungu wa Yakobo.   
10 Ndidzadula nyanga za onse oyipa  
koma nyanga za olungama zidzakwezedwa.