Salimo 67
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Salimo. 
 
1 Yehova atikomere mtima ndi kutidalitsa,  
achititse kuti nkhope yake itiwalire.   
2 Kuti njira zanu zidziwike pa dziko lapansi,  
chipulumutso chanu pakati pa mitundu yonse.   
   
 
3 Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu;  
mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.   
4 Mitundu yonse ya anthu isangalale ndi kuyimba mwachimwemwe,  
pakuti inu mumaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo  
ndi kutsogolera mitundu ya anthu a dziko lapansi.   
5 Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu;  
mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.   
   
 
6 Nthaka yabereka zokolola zake;  
tidalitseni Mulungu wathu.   
7 Mulungu atidalitse  
kuti pamenepo malekezero onse a dziko lapansi apembedze Iyeyo.