Salimo 6
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Molingana ndi seminiti. Salimo la Davide. 
 
1 Inu Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu,  
kapena kundilanga mu ukali wanu.   
2 Ndichitireni chifundo Inu Yehova, pakuti ndalefuka;  
Inu Yehova chiritseni, pakuti mafupa anga ali pa ululu waukulu.   
3 Moyo wanga uli pa mazunzo aakulu.  
Mpaka liti, Inu Yehova, mpaka liti?   
   
 
4 Tembenukani Inu Yehova, ndipo mundilanditse;  
pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.   
5 Palibe amene amakukumbukirani pamene wamwalira;  
Amakutamandani ndani ali ku manda?   
   
 
6 Ine ndatopa ndi kubuwula;  
usiku wonse pa bedi panga pamadzaza ndi misozi yanga;  
ndimanyowetsa pogona panga ndi misozi.   
7 Maso anga atupa chifukwa cha chisoni;  
akulephera kuona chifukwa cha adani anga.   
   
 
8 Chokani kwa ine inu nonse amene mumachita zoyipa,  
pakuti Yehova wamva kulira kwanga.   
9 Yehova wamva kupempha kwanga kofuna chifundo;  
Yehova walandira pemphero langa.   
10 Adani anga onse adzachita manyazi ndipo adzakhala ndi mantha;  
adzabwerera msangamsanga mwa manyazi.