Salimo 143
Salimo la Davide. 
 
1 Yehova imvani pemphero langa,  
mvetserani kulira kwanga kopempha chifundo;  
mwa kukhulupirika kwanu ndi chilungamo chanu  
bwerani kudzandithandiza.   
2 Musazenge mlandu mtumiki wanu,  
pakuti palibe munthu wamoyo amene ndi wolungama pamaso panu.   
   
 
3 Mdani akundithamangitsa,  
iye wandipondereza pansi;  
wachititsa kuti ndikhale mu mdima  
ngati munthu amene anafa kale.   
4 Choncho mzimu wanga ukufowoka mʼkati mwanga;  
mʼkati mwanga, mtima wanga uli ndi nkhawa.   
   
 
5 Ndimakumbukira masiku amakedzana;  
ndimalingalira za ntchito yanu yonse,  
ndimaganizira zimene manja anu anachita.   
6 Ndatambalitsa manja anga kwa Inu;  
moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu monga nthaka yowuma.  
Sela
   
   
 
7 Yehova ndiyankheni msanga;  
mzimu wanga ukufowoka.  
Musandibisire nkhope yanu,  
mwina ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje.   
8 Lolani kuti mmawa ubweretse mawu achikondi chanu chosasinthika,  
pakuti ine ndimadalira Inu.  
Mundisonyeze njira yoti ndiyendemo,  
pakuti kwa Inu nditukulira moyo wanga.   
9 Pulumutseni kwa adani anga, Inu Yehova,  
pakuti ndimabisala mwa Inu.   
10 Phunzitseni kuchita chifuniro chanu,  
popeza ndinu Mulungu wanga;  
Mzimu wanu wabwino unditsogolere  
pa njira yanu yosalala.   
   
 
11 Sungani moyo wanga Inu Yehova chifukwa cha dzina lanu;  
mwa chilungamo chanu tulutseni mʼmasautso anga.   
12 Mwa chikondi chanu chosasinthika khalitsani chete adani anga;  
wonongani adani anga,  
pakuti ndine mtumiki wanu.