Salimo 141
Salimo la Davide. 
 
1 Inu Yehova ndikukuyitanani; bwerani msanga kwa ine.  
Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu.   
2 Pemphero langa lifike kwa Inu ngati lubani;  
kukweza manja kwanga kukhale ngati nsembe yamadzulo.   
   
 
3 Yehova ikani mlonda pakamwa panga;  
londerani khomo la pa milomo yanga.   
4 Musalole kuti mtima wanga ukokedwere ku zoyipa;  
kuchita ntchito zonyansa  
pamodzi ndi anthu amene amachita zoyipa;  
musalole kuti ndidye nawo zokoma zawo.   
   
 
5 Munthu wolungama andikanthe, chimenecho ndiye chifundo;  
andidzudzule ndiye mafuta pa mutu wanga.  
Mutu wanga sudzakana zimenezi.  
   
 
Komabe pemphero langa nthawi zonse ndi lotsutsana ndi ntchito za anthu ochita zoyipa.   
6 Olamulira awo adzaponyedwa pansi kuchokera pa malo okwera kwambiri,  
ndipo anthu oyipa adzaphunzira kuti mawu anga anayankhulidwa bwino.   
7 Iwo adzati, “Monga momwe nkhuni zimamwazikira akaziwaza,  
ndi momwenso mafupa athu amwazikira pa khomo la manda.”   
   
 
8 Koma maso anga akupenyetsetsa Inu Ambuye Wamphamvuzonse;  
ndimathawira kwa Inu, musandipereke ku imfa.   
9 Mundipulumutse ku misampha imene anditchera,  
ku makhwekhwe amene anthu oyipa andikonzera.   
10 Anthu oyipa akodwe mʼmaukonde awo,  
mpaka ine nditadutsa mwamtendere.