9
Za Nzeru ndi Uchitsiru
Nzeru inamanga nyumba yake;
inayimika nsanamira zake zisanu ndi ziwiri.
Inapha ziweto zake ndipo yasakaniza vinyo wake;
inasakaniza vinyo wake ndi kuyala tebulo lake.
Nzeruyo inatuma adzakazi ake,
kuti akakhale pamwamba penipeni pa mzinda ndi kukalengeza kuti,
“Aliyense amene ali munthu wamba, abwere kuno!”
Kwa onse opanda nzeru inkanena kuti,
“Bwerani, dzadyeni chakudya changa
ndipo dzamweni vinyo amene ndakonza.
Lekani zopusa zanu kuti mukhale ndi moyo;
yendani njira ya nzeru yomvetsa zinthu.”
 
Aliyense amene amayesa kukonza munthu wonyoza amadziputira minyozo;
aliyense amene amadzudzula munthu woyipa amadetsa mbiri yake.
Usadzudzule munthu wonyoza kuti angadzadane nawe;
dzudzula munthu wanzeru ndipo adzakukonda.
Ukalangiza munthu wanzeru ndiye adzapitirira kukhala wanzeru;
ukaphunzitsa munthu wolungama ndiye adzawonjezera kuphunzira kwake.
 
10 Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru;
kudziwa Woyerayo ndiko kukhala womvetsa bwino zinthu.
11 Chifukwa cha ine nzeru, masiku ako adzachuluka,
ndipo zaka za moyo wako zidzawonjezeredwa.
12 Ngati ndiwe wanzeru, nzeru yakoyo idzakupindulitsa;
ngati ndiwe wonyoza ena, udzavutika wekha.
 
13 Uchitsiru ndi mkazi waphokoso,
wopulikira ndiponso wosadziwa zinthu.
14 Iye amakhala pa mpando, pa khomo la nyumba yake,
pamalo aatali a mu mzinda,
15 kuti aziyitana anthu ongodutsa,
amene akunka nayenda njira zawo.
16 Amati, “Onse amene ndi anthu wamba abwere kuno,”
ndipo kwa wopanda nzeru amati,
17 “Madzi akuba ndiye amatsekemera;
chakudya chodya mobisa ndi chokoma!”
18 Koma amunawo sadziwa kuti akufa ali kale komweko,
ndi kuti alendo ake alowa kale mʼmanda akuya.