7
Za Mkazi Wachigololo
Mwana wanga, mvera mawu anga;
usunge bwino malamulo angawa.
Utsate malamulo anga ndipo udzakhala ndi moyo;
samala malangizo angawa monga uchitira ndi maso ako.
Uchite ngati wawamangirira pa zala zako,
ndiponso ngati kuti wawalemba pa mtima pako.
Nzeru uyiwuze kuti, “Iwe ndiwe mlongo wanga,”
ndipo khalidwe lomvetsa bwino zinthu ulitchule kuti, “Bwenzi langa lapamtima.”
Zidzakuteteza kwa mkazi wachigololo
ndiponso zidzakuthandiza kusamvera mawu oshashalika a mkazi wachilendo.
 
Tsiku lina pa zenera la nyumba yanga
ndinasuzumira pa zenera.
Ndinaona pakati pa anthu opusa,
pakati pa anyamata,
mnyamata wina wopanda nzeru.
Iye ankayenda njira yodutsa pafupi ndi nyumba ya mkaziyo,
kuyenda molunjika nyumba ya mkaziyo.
Inali nthawi yachisisira madzulo,
nthawi ya usiku, kuli mdima.
 
10 Ndipo mkaziyo anadzakumana naye,
atavala ngati munthu wachiwerewere wa mtima wonyenga.
11 (Mkaziyo ndi wolongolola ndiponso nkhutukumve,
iye ndi wosakhazikika pa khomo.
12 Mwina umupeza pa msewu, mwina umupeza pa msika,
ndipo amadikirira munthu pa mphambano iliyonse).
13 Tsono amagwira mnyamatayo ndi kupsompsona
ndi nkhope yake yopanda manyazi amamuwuza kuti,
 
14 “Ndinayenera kupereka nsembe zachiyanjano.
Lero ndakwaniritsa malumbiro anga.
15 Choncho ndinabwera kudzakumana nawe;
ndinkakufunafuna ndipo ndakupeza!
16 Pa bedi panga ndayalapo
nsalu zosalala zokongola zochokera ku Igupto.
17 Pa bedi panga ndawazapo zonunkhira
za mure, mafuta onunkhira a aloe ndi sinamoni.
18 Bwera, tiye tikhale malo amodzi kukondwerera chikondi mpaka mmawa;
tiye tisangalatsane mwachikondi!
19 Mwamuna wanga kulibe ku nyumbako;
wapita ulendo wautali:
20 Anatenga thumba la ndalama
ndipo adzabwera ku nyumba mwezi ukakhwima.”
 
21 Ndi mawu ake onyengerera amamukakamiza mnyamatayo;
amukopa ndi mawu ake oshashalika.
22 Nthawi yomweyo chitsiru chimamutsatira mkaziyo
ngati ngʼombe yopita kukaphedwa,
monga momwe mbawala ikodwera mu msampha,
23 mpaka muvi utalasa chiwindi chake,
chimakhala ngati mbalame yothamangira mʼkhwekhwe,
osadziwa kuti moyo wake uwonongeka.
 
24 Tsono ana inu, ndimvereni;
mvetsetsani zimene ndikunena.
25 Musatengeke mtima ndi njira za mkazi ameneyu;
musasochere potsata njira zake.
26 Paja iye anagwetsa anthu ambiri;
wapha gulu lalikulu la anthu.
27 Nyumba yake ndi njira yopita ku manda,
yotsikira ku malo a anthu akufa.