23
1 Ngati ukhala pansi kuti udye pamodzi ndi wolamulira,  
uyangʼane bwino zimene zili pamaso pako,   
2 ngati ndiwe munthu wadyera  
udziletse kuti usaonetse dyera lakolo.   
3 Usasirire zakudya zake,  
pakuti zimenezo ndi zakudya zachinyengo.   
   
 
4 Usadzitopetse wekha ndi kufuna chuma,  
ukhale ndi nzeru ya kudziretsa.   
5 Ukangoti wachipeza chumacho uwona posachedwa kuti palibepo.  
Chumacho chimachita ngati chamera mapiko mwadzidzidzi  
ndi kuwuluka kunka kumwamba ngati chiwombankhanga.   
   
 
6 Usadye chakudya cha munthu waumbombo,  
usalakalake zakudya zake zokoma;   
7 paja iye ndi munthu amene  
nthawi zonse amaganizira za mtengo wake  
ngakhale amati kwa iwe, “Idya ndi kumwa,”  
koma sakondweretsedwa nawe.   
8 Udzasanza zimene wadyazo  
ndipo mawu ako woyamikira adzapita pachabe.   
   
 
9 Usayankhule munthu wopusa akumva,  
pakuti adzanyoza mawu ako anzeru.   
   
 
10 Usasunthe mwala wa mʼmalire akalekale  
kapena kulowerera mʼminda ya ana amasiye,   
11 paja Mpulumutsi wawo ndi wamphamvu;  
iye adzawateteza pa milandu yawo kutsutsana nawe.   
   
 
12 Mtima wako uzikhala pa malangizo  
ndipo makutu ako azimvetsera mawu a chidziwitso.   
   
 
13 Usaleke kumulangiza mwana;  
ngati umulanga ndi chikwapu sadzafa.   
14 Ukamukwapula ndi tsatsa  
udzapulumutsa moyo wake.   
   
 
15 Mwana wanga, ngati mtima wako ukhala wanzeru,  
inenso mtima wanga udzakondwera.   
16 Mtima wanga udzakondwera  
pamene ndidzakumva ukuyankhula zolungama.   
   
 
17 Mtima wako usachite nsanje ndi anthu ochimwa,  
koma uziopa Yehova tsiku ndi tsiku.   
18 Ndithu za mʼtsogolo zilipo  
ndipo chiyembekezo chakocho sichidzalephereka.   
   
 
19 Tamvera mwana wanga, ndipo ukhale wanzeru,  
mtima wako uwuyendetse mʼnjira yabwino.   
20 Usakhale pakati pa anthu amene amaledzera  
kapena pakati pa anthu amene amadya nyama mwadyera.   
21 Paja anthu oledzera ndi adyera amadzakhala amphawi  
ndipo aulesi adzavala sanza.   
   
 
22 Mvera abambo ako amene anakubala,  
usanyoze amayi ako pamene akalamba.   
23 Gula choonadi ndipo usachigulitse;  
ugulenso nzeru, mwambo ndiponso kumvetsa zinthu bwino.   
24 Abambo a munthu wolungama ali ndi chimwemwe chachikulu;  
Wobala mwana wanzeru adzakondwera naye.   
25 Abambo ndi amayi ako asangalale;  
amene anakubereka akondwere!   
   
 
26 Mwana wanga, undikhulupirire  
ndipo maso ako apenyetsetse njira zanga.   
27 Paja mkazi wachiwerewere ali ngati dzenje lozama;  
ndipo mkazi woyendayenda ali ngati chitsime chopapatiza.   
28 Amabisala ngati mbala yachifwamba,  
ndipo amuna amakhala osakhulupirika chifukwa cha iyeyu.   
   
 
29 Ndani ali ndi tsoka? Ndani ali ndi chisoni?  
Ndani ali pa mkangano? Ndani ali ndi madandawulo?  
Ndani ali ndi zipsera zosadziwika uko zachokera? Ndani ali ndi maso ofiira?   
30 Ndi amene amakhalitsa pa mowa,  
amene amapita nalawa vinyo osakanizidwa.   
31 Usatengeke mtima ndi kufiira kwa vinyo,  
pamene akuwira mʼchikho  
pamene akumweka bwino!   
32 Potsiriza pake amaluma ngati njoka,  
ndipo amajompha ngati mphiri.   
33 Maso ako adzaona zinthu zachilendo  
ndipo maganizo ndi mawu ako adzakhala osokonekera.   
34 Udzakhala ngati munthu amene ali gone pakati pa nyanja,  
kapena ngati munthu wogona pa msonga ya mlongoti ya ngalawa.   
35 Iwe udzanena kuti, “Anandimenya, koma sindinapwetekedwe!  
Andimenya koma sindinamve kanthu!  
Kodi ndidzuka nthawi yanji?  
Ndiye ndifunefunenso vinyo wina.”