21
Mtima wa mfumu uli ngati mtsinje wamadzi mʼdzanja la Yehova;
Iye amautsongolera pa chilichonse chimene akufuna.
 
Makhalidwe a munthu amaoneka olungama kwa mwini wakeyo,
koma Yehova ndiye amayesa mtima wake.
 
Za chilungamo ndi zolondola
ndi zomwe zimakondweretsa Yehova kuposa kupereka nsembe.
 
Maso odzikuza ndi mtima wonyada,
zimatsogolera anthu oyipa ngati nyale nʼchifukwa chake amachimwa.
 
Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa zinthu zake;
koma aliyense wochita zinthu mofulumira amadzakhala wosauka.
 
Chuma chochipeza ndi mawu onyenga ndi chosakhalitsa
ndipo chimakola anthu mu msampha wa imfa.
 
Chiwawa cha anthu oyipa chidzawawononga,
pakuti iwo amakana kuchita zolungama.
 
Njira ya munthu wolakwa ndi yokhotakhota,
koma makhalidwe a munthu wosalakwa ndi olungama.
 
Nʼkwabwino kukhala wekha pa ngodya ya denga la nyumba,
kuposa kukhala mʼnyumba pamodzi ndi mkazi wolongolola.
 
10 Munthu woyipa amalakalaka zoyipa;
sachitira chifundo mnansi wake wovutika.
 
11 Munthu wonyoza akalangidwa, anthu opusa amapeza nzeru;
koma munthu wanzeru akalangizidwa, amapeza chidziwitso.
 
12 Zolingalira za munthu woyipa nʼzosabisika pamaso pa Yehova,
ndipo Iye adzawononga woyipayo.
 
13 Amene atsekera mʼkhutu mwake wosauka akamalira,
nayenso adzalira koma palibe adzamuyankhe.
 
14 Mphatso yoperekedwa mseri imathetsa mkwiyo,
ndipo chiphuphu choperekedwa mobisa chimathetsa mphamvu ya ukali woopsa.
 
15 Chilungamo chikachitika anthu olungama amasangalala,
koma anthu oyipa amaopsedwa nazo.
 
16 Munthu amene amachoka pa njira ya anthu anzeru
adzapezeka mʼgulu la anthu akufa.
 
17 Aliyense wokonda zisangalalo adzasanduka mʼmphawi,
ndipo wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.
 
18 Anthu oyipa adzakhala chowombolera cha anthu olungama
ndipo osakhulupirika chowombolera anthu olungama mtima.
 
19 Nʼkwabwino kukhala mʼchipululu
kuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wopsa mtima msanga.
 
20 Munthu wanzeru samwaza chuma chake,
koma wopusa amachiwononga.
 
21 Amene amatsata chilungamo ndi kukhulupirika,
amapeza moyo ndi ulemerero.
 
22 Munthu wanzeru amagonjetsa mzinda wa anthu amphamvu
ndi kugwetsa linga limene iwo amalidalira.
 
23 Amene amagwira pakamwa pake ndi lilime lake
sapeza mavuto.
 
24 Munthu wonyada ndi wodzikuza amamutcha, “Mnyodoli,”
iye amachita zinthu modzitama kwambiri.
 
25 Chilakolako cha munthu waulesi chidzamupha yekha
chifukwa manja ake amangokhala goba osagwira ntchito.
26 Tsiku lonse anthu oyipa amasirira zambiri,
koma anthu olungama amapereka mowolowamanja.
 
27 Nsembe ya anthu oyipa imamunyansa Yehova,
nanji akayipereka ndi cholinga choyipa!
 
28 Mboni yonama idzawonongeka,
koma mawu a munthu wakumva adzakhala nthawi zonse.
 
29 Munthu woyipa amafuna kudzionetsa ngati wolimba mtima,
koma munthu wowongoka amaganizira njira zake.
 
30 Palibe nzeru, palibe kumvetsa bwino, palibenso uphungu,
zimene zingapambane Yehova.
 
31 Kavalo amamukonzera tsiku la nkhondo,
koma ndi Yehova amene amapambanitsa.