18
Munthu wokonda kukhala yekha amafunafuna zomukomera yekha;
iye amatsutsana ndi malangizo onse anzeru.
 
Chitsiru chilibe chidwi chomvetsa zinthu,
koma chimakondwera ndi kuyankhula maganizo ake okha.
 
Kuyipa mtima kukabwera, manyozonso amabwera.
Manyazi amabwera pamodzi ndi kunyozeka.
 
Mawu a munthu ali ngati madzi akuya,
kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wotumphuka.
 
Si kwabwino kukondera munthu woyipa pa milandu;
kapena kupondereza munthu wosalakwa.
 
Mawu a chitsiru amautsa mkangano;
pakamwa pake pamayitana mkwapulo.
 
Pakamwa pa chitsiru ndipo pamabweretsa chiwonongeko chake,
ndipo milomo yake ili ngati msampha wa moyo wake.
 
Mawu a miseche ali ngati chakudya chokoma;
amalowa mʼmimba mwa munthu.
 
Munthu waulesi pa ntchito yake
ali pachibale ndi munthu amene amawononga zinthu.
 
10 Dzina la Yehova lili ngati nsanja yolimba;
wolungama amathawiramo napulumuka.
 
11 Chuma cha anthu olemera chili ngati mzinda wake wolimba;
chili ngati khoma lalitali limene amaganiza kuti limutchinjiriza.
 
12 Chiwonongeko chisanafike, mtima wa munthu umakhala wonyada,
koma ulemu umatsatira kudzichepetsa.
 
13 Ukayankha usanamvetse bwino nkhani,
umenewo ndi uchitsiru ndipo umachita manyazi.
 
14 Mtima wa munthu utha kupirira pa matenda,
koma munthu akataya mtima ndani angathe kumulimbitsanso.
 
15 Munthu wanzeru amawonjezera nzeru zina;
amafunafuna kudziwa bwino zinthu.
 
16 Mphatso ya munthu imamutsekulira njira
yomufikitsa pamaso pa anthu akuluakulu.
 
17 Amene amayamba kufotokoza mlandu wake amaoneka ngati wolungama ndiye
mpaka mnzake atabwera ndi kumufunsa bwino.
 
18 Kuchita maere kumathetsa mikangano;
amalekanitsa okangana amphamvu.
 
19 Mʼbale amene wamuthandiza amakhala ngati mzinda wolimba,
koma kukangana naye kumatsekereza thandizo.
 
20 Munthu amapeza bwino malingana ndi zoyankhula zake.
Adzakhuta ndi zipatso za pakamwa pake.
 
21 Mawu ako angathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo.
Wokonda kuyankhulayankhula adzadya zipatso zake.
 
22 Wapeza mkazi wapeza chinthu chabwino
ndipo Yehova amamukomera mtima.
 
23 Munthu wosauka amapempha
koma munthu wolemera amayankha mwaukali.
 
24 Pali abwenzi amene chibwenzi chawo nʼchapamaso,
koma pali bwenzi limene limakukangamira kuposa mʼbale wako.