34
Malire a Dziko la Kanaani
1 Yehova anawuza Mose kuti,
2 “Lamula Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Pamene mulowa mʼdziko la Kanaani, dziko lomwe lidzaperekedwa kwa inu ngati cholowa chanu, lidzakhale ndi malire awa:
3 “ ‘Chigawo cha kummwera kwa dziko lanu chidzayambira ku chipululu cha Zini motsatana ndi malire a Edomu. Kummawa malire anu a kummwera adzayambira kummawa, kumathero a Nyanja ya Mchere.
4 Malirewo adzapita kummwera ndipo adzakwera phiri la Akirabimu mpaka ku Zini. Mathero ake adzakhala kummwera kwa Kadesi-Baranea. Ndipo adzapitenso ku Hazari Adari mpaka kukafika ku Azimoni,
5 kumene malirewo adzakhote kuchokera ku Azimoni mpaka ku khwawa la ku Igupto ndi kukathera ku Nyanja Yayikulu.
6 “ ‘Malire anu a ku madzulo adzakhala ku gombe la Nyanja Yayikulu. Amenewo ndiwo adzakhale malire anu a ku madzulo.
7 “ ‘Malire anu a kumpoto, mzere wake uyambire ku Nyanja Yayikulu mpaka ku phiri la Hori
8 ndi kuchokera ku phiri la Hori mpaka ku Lebo Hamati. Malirewa apite ku Zedadi,
9 ndi kupitirira mpaka ku Ziforoni ndi kukathera ku Hazari-Enani. Awa ndiwo adzakhale malire anu a kumpoto.
10 “ ‘Za malire anu a kummawa, mulembe mzere kuchokera ku Hazari-Enani mpaka kukafika ku Sefamu.
11 Malirewo adzatsikire ku Sefamu mpaka ku Ribila cha kummawa kwa Aini ndi kupitirira mpaka ku matsitso a cha kummawa kwa Nyanja ya Kinereti.
12 Tsono malirewo adzatsika motsatana ndi Yorodani ndi kukathera ku Nyanja ya Mchere.
“ ‘Limeneli lidzakhala dziko lanu ndi malire ake mbali zonse.’ ”
13 Ndipo Mose analamula Aisraeli kuti, “Limeneli ndi dziko limene mudzalilandira pochita maere kuti likhale cholowa chanu. Yehova analamula kuti liperekedwe ku mafuko asanu ndi anayi ndi theka,
14 chifukwa mabanja a fuko la Rubeni, fuko la Gadi, ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo.
15 Mafuko awiriwa pamodzi ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo patsidya pa mtsinje wa Yorodani ku Yeriko cha kummawa kotulukira dzuwa.”
16 Yehova anawuza Mose kuti,
17 “Awa ndi mayina a anthu amene adzakugawireni dzikoli kuti likhale cholowa chanu: wansembe Eliezara ndi Yoswa mwana wa Nuni.
18 Musankhe mtsogoleri mmodzi kuchokera ku fuko lililonse kuti athandize kugawa dzikolo.
19 Mayina awo ndi awa:
Kalebe mwana wa Yefune,
wochokera ku fuko la Yuda,
20 Semueli mwana wa Amihudi,
wochokera ku fuko la Simeoni;
21 Elidadi mwana wa Kisiloni,
wochokera ku fuko la Benjamini;
22 Buki mwana wa Yogili,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Dani;
23 Hanieli mwana wa Efodi,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Manase, mwana wa Yosefe;
24 Kemueli mwana wa Sifitani,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Efereimu, mwana wa Yosefe.
25 Elizafani mwana wa Parinaki,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Zebuloni;
26 Palitieli mwana wa Azani,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Isakara,
27 Ahihudi mwana wa Selomi,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Aseri;
28 Pedaheli mwana wa Amihudi,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Nafutali.”
29 Awa ndiwo mayina a anthu amene Yehova analamula kuti agawe cholowa cha Aisraeli mʼdziko la Kanaani.