4
Yesu Ayesedwa Mʼchipululu
1 Pambuyo pake Yesu anatsogozedwa ndi Mzimu Woyera kupita ku chipululu kukayesedwa ndi mdierekezi.
2 Ndipo atasala kudya masiku makumi anayi usana ndi usiku, anamva njala.
3 Woyesayo anadza kwa Iye nati, “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, sandutsani miyala iyi kuti ikhale buledi.”
4 Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa, ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Mulungu.’ ”
5 Pamenepo mdierekezi anapita naye ku mzinda woyera namuyimiritsa pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu.
6 Ndipo anati, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, dziponyeni nokha pansi. Pakuti kwalembedwa:
“ ‘Adzalamulira angelo ake za iwe,
ndipo adzakunyamula ndi manja awo
kuti phazi lako lisagunde pa mwala.’ ”
7 Yesu anamuyankha kuti, “Kwalembedwanso: ‘Musamuyese Yehova Mulungu wanu.’ ”
8 Kenaka mdierekezi anamutengera Yesu ku phiri lalitali kwambiri namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi ndi ulemerero wawo.
9 Ndipo anati kwa Iye, “Zonsezi ndidzakupatsani ngati mutandiweramira ndi kundipembedza ine.”
10 Yesu anati kwa iye, “Choka Satana! Zalembedwa, ‘Pembedza Yehova Mulungu wako ndi kumutumikira Iye yekha.’ ”
11 Pamenepo mdierekezi anamusiya ndipo angelo anamutumikira Iye.
Yesu Ayamba Kulalikira
12 Yesu atamva kuti Yohane anamutsekera mʼndende, anabwerera ku Galileya.
13 Ndipo atachoka ku Nazareti anapita ku Kaperenawo ndi kukhala mʼmbali mwa nyanja, mʼdera la Zebuloni ndi Nafutali;
14 pokwaniritsa zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yesaya kuti,
15 “Dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali,
njira ya ku nyanja, kutsidya lija la Yorodani,
Galileya wa anthu a mitundu ina,
16 anthu okhala mu mdima
awona kuwala kwakukulu;
ndi kwa iwo okhala mʼdziko la mthunzi wa imfa
kuwunika kwawafikira.”
17 Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikira nati, “Tembenukani mtima ufumu wakumwamba wayandikira.”
Yesu Ayitana Ophunzira ake Oyamba
18 Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wotchedwa Petro ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja popeza anali asodzi.
19 Yesu anati, “Bwerani, tsateni Ine ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.”
20 Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye.
21 Atapita patsogolo, anaona abale ena awiri, Yakobo ndi mʼbale wake Yohane ana a Zebedayo. Iwowa anali mʼbwato ndi abambo awo, Zebedayo, akukonza makoka awo ndipo Yesu anawayitana.
22 Nthawi yomweyo anasiya bwato ndi abambo awo namutsata Iye.
Yesu Achiritsa Odwala
23 Yesu anayendayenda mu Galileya kuphunzitsa mʼmasunagoge awo, nalalikira Uthenga Wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa matenda onse pakati pa anthu.
24 Mbiri yake yonse inawanda ku Siriya konse ndipo anthu anabweretsa kwa Iye onse amene anali odwala nthenda zosiyanasiyana, womva maululu aakulu, ogwidwa ndi ziwanda, odwala matenda akugwa ndi olumala ndipo Iye anawachiritsa.
25 Magulu ambiri a anthu anachokera ku Galileya, Dekapoli, Yerusalemu, Yudeya ndi ku madera a kutsidya la mtsinje wa Yorodani namutsata Iye.