14
Kuphedwa kwa Yohane Mʼbatizi
1 Pa nthawi imeneyo Mfumu Herode anamva za mbiri ya Yesu.
2 Ndipo iye anati kwa antchito ake, “Uyu ndi Yohane Mʼbatizi; iye wauka kwa akufa! Ichi ndi chifukwa chake mphamvu zodabwitsa zikugwira ntchito mwa iye.”
3 Pakuti Herode anamugwira Yohane ndi kumumanga ndipo anamuyika mʼndende chifukwa cha Herodia mkazi wa mʼbale wake Filipo.
4 Chifukwa Yohane anakhala akunena kwa iye kuti, “Sichololedwa kwa inu kutenga mkaziyo.”
5 Herode anafuna kupha Yohane koma iye anaopa anthu chifukwa anamuyesa iye mneneri.
6 Pa tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodia anavina pamaso pa anthu ndipo anasangalatsa kwambiri.
7 Kotero Herode analonjeza ndi lumbiro kumupatsa chilichonse chimene mwanayo angamupemphe.
8 Ndipo atamupangira amayi ake anati, “Mundipatse pomwe pano mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale.”
9 Mfumuyo inamva chisoni koma chifukwa cha lumbiro lake ndi alendo amene anali pa phwando lake analamulira kuti chofuna chake chipatsidwe;
10 ndipo anakadula mutu wa Yohane mʼndende.
11 Mutu wake anawubweretsa mʼmbale ndi kumupatsa mtsikanayo amene anawutengera kwa amayi ake.
12 Ophunzira a Yohane anabwera nadzatenga mtembo wake ndi kukawuyika mʼmanda. Pomwepo iwo anapita kukamuwuza Yesu.
Yesu Adyetsa Anthu 5,000
13 Yesu atamva zimene zinachitika, anachoka pa bwato mwachinsinsi kupita kumalo a yekha. Magulu a anthu atamva izi anamutsatira Iye poyenda pansi kuchokera ku mizinda.
14 Yesu atafika ku mtunda, ndi kuona gulu lalikulu la anthu, Iye anamva nawo chifundo ndipo anachiritsa odwala awo.
15 Kutayamba mdima, ophunzira anabwera kwa Iye nati, “Kuno ndi kutchire ndipo kwayamba kale kuda. Awuzeni anthu azipita kuti afike ku midzi ndi kukadzigulira zakudya.”
16 Yesu anawayankha kuti, “Sikofunika kuti azipita. Inuyo muwapatse kanthu kuti adye.”
17 Iwo anayankha kuti, “Tili ndi malofu asanu okha a buledi ndi nsomba ziwiri.”
18 Koma Iye anati, “Bweretsani kwa Ine.”
19 Analamula anthu kuti akhale pansi pa udzu ndipo anatenga buledi musanu ndi nsomba ziwiri nayangʼana kumwamba, nayamika nagawa bulediyo. Kenaka anapereka bulediyo kwa ophunzira ake ndipo ophunzirawo anagawira anthu.
20 Onse anadya nakhuta ndipo ophunzira anatola zotsalira ndi kudzaza madengu khumi ndi awiri.
21 Chiwerengero cha amene anadya kupatulako amayi ndi ana chinali pafupifupi amuna 5,000.
Yesu Ayenda pa Nyanja
22 Nthawi yomweyo anawawuza ophunzira ake kuti alowe mʼbwato ndi kuti atsogole kupita kutsidya lina pamene Iye ankawuza anthu kuti azipita kwawo.
23 Atatha kuwawuza kuti azipita kwawo, Iye anakwera ku phiri yekha kukapemphera. Pamene kumada anali kumeneko yekha.
24 Pamenepo nʼkuti bwato litapita patali pangʼono kuchokera ku mtunda ndipo linavutika ndi mafunde chifukwa mphepo inkawomba mokumana nalo.
25 Pa ora lachinayi usiku, Yesu anabwera kwa iwo akuyendabe pa nyanja.
26 Ophunzira atamuona akuyenda pa nyanja, anaopa nati, “Ndi mzukwa!” Ndipo analira chifukwa cha mantha.
27 Koma Yesu nthawi yomweyo anawawuza kuti, “Limbani mtima! Ndine, musaope.”
28 Petro anayankha nati, “Ambuye ngati ndinu, mundiwuze ndibwere kuli inuko pa madzipo.”
29 Iye anati, “Bwera.”
Pamenepo Petro anatuluka mʼbwato ndipo anayenda pa madzi kupita kwa Yesu.
30 Koma ataona mphepo, iye anachita mantha ndipo anayamba kumira, nafuwula nati, “Ambuye ndipulumutseni!”
31 Ndipo mofulumira Yesu anatambasula dzanja lake namugwira iye, nati, “Iwe wachikhulupiriro chochepa, bwanji unakayika?”
32 Ndipo atalowa mʼbwato mphepo inaleka.
33 Pamenepo amene anali mʼbwato anamulambira Iye, nati, “Zoonadi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.”
34 Atawoloka, anafika ku Genesareti.
35 Anthu akumeneko atamuzindikira Yesu, iwo anatumiza mawu kwa onse ozungulira deralo. Anthu anabwera ndi odwala awo onse kwa Iye.
36 Ndipo anamupempha alole kuti akhudze mphonje ya mkanjo wake, ndipo onse amene anamukhudza anachiritsidwa.