2
Zokonzekera za Munthu ndi Zokonzekera za Mulungu 
 
1 Tsoka kwa amene amakonzekera chiwembu,  
kwa amene amakonzekera kuchita zoyipa usiku pa mabedi awo!  
Kukacha mmawa amakachitadi  
chifukwa ali ndi mphamvu zochitira zimenezo.   
2 Amasirira minda ndi kuyilanda,  
amasirira nyumba ndi kuzilanda.  
Amatenga nyumba ya munthu mwachinyengo,  
munthu mnzawo kumulanda cholowa chake.   
3 Nʼchifukwa chake Yehova akuti,  
“Ine ndikukonzekera kubweretsa tsoka pa anthu awa,  
tsoka limene simudzatha kudzipulumutsa nokha.  
Inu simudzayendanso monyada,  
pakuti idzakhala nthawi ya masautso.   
4 Tsiku limenelo anthu adzakuchitani chipongwe;  
adzakunyogodolani ndi nyimbo iyi yamaliro:  
‘Tawonongeka kotheratu;  
dziko la anthu anga lagawidwa.  
Iye wandilanda!  
Wapereka minda yathu kwa anthu otiwukira.’ ”   
   
 
5 Nʼchifukwa chake simudzakhala ndi munthu mu msonkhano wa Yehova  
kuti agawe dziko pochita maere.   
Aneneri Onyenga 
 
6 Aneneri awo amanena kuti, “Usanenere!  
Usanenere ndi pangʼono pomwe zimenezi;  
ife sitidzachititsidwa manyazi.”   
7 Inu nyumba ya Yakobo, monga zimenezi ndi zoyenera kuzinena:  
“Kodi Mzimu wa Yehova wakwiya?  
Kodi Iye amachita zinthu zotere?”  
   
 
“Kodi mawu ake sabweretsa zabwino  
kwa amene amayenda molungama?   
8 Posachedwapa anthu anga andiwukira  
ngati mdani.  
Mumawavula mkanjo wamtengowapatali  
anthu amene amadutsa mosaopa kanthu,  
monga anthu amene akubwera ku nkhondo.   
9 Mumatulutsa akazi a anthu anga  
mʼnyumba zawo zabwino.  
Mumalanda ana awo madalitso anga  
kosatha.   
10 Nyamukani, chokani!  
Pakuti ano si malo anu opumulirapo,  
chifukwa ayipitsidwa,  
awonongedwa, sangatheke kuwakonzanso.   
11 Ngati munthu wabodza ndi wachinyengo abwera nʼkunena kuti,  
‘Ine ndidzanenera ndipo mudzakhala ndi vinyo ndi mowa wambiri,  
woteroyo adzakhala mneneri amene anthu awa angamukonde!’   
Alonjeza Chipulumutso 
 
12 “Inu banja la Yakobo, ndidzakusonkhanitsani nonse;  
ndidzawasonkhanitsa pamodzi otsala a ku Israeli.  
Ndidzawabweretsa pamodzi ngati nkhosa mʼkhola,  
ngati ziweto pa msipu wake;  
malowo adzadzaza ndi chinamtindi cha anthu.   
13 Amene adzawapulumutse adzayenda patsogolo pawo;  
iwo adzathyola chipata ndipo adzatuluka.  
Mfumu yawo idzawatsogolera,  
Yehova adzakhala patsogolo pawo.”