24
Mafuta ndi Buledi wa Pamaso pa Yehova
1 Yehova anawuza Mose kuti,
2 “Lamula Aisraeli kuti akupatse mafuta anyale, a olivi wabwino kwambiri kuti nyalezo ziziyaka nthawi zonse.
3 Kunja kwa nsalu yotchinga Bokosi la Chipangano, mʼchihema cha msonkhano, Aaroni azionetsetsa kuti nyale ikukhala chiyakire pamaso pa Yehova kuyambira madzulo mpaka mmawa, nthawi zonse. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yonse.
4 Aaroni ayatse nyale zimene zili pa choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri kuti zikhale zoyaka nthawi zonse pamaso pa Yehova.
5 “Mutenge ufa wosalala ndipo muphike makeke khumi ndi awiri ndipo keke iliyonse ikhale ya ufa wa makilogalamu awiri.
6 Muwayike pa tebulo la golide wabwino kwambiri pamaso pa Yehova mʼmizere iwiri. Mzere uliwonse ukhale wa makeke asanu ndi imodzi.
7 Pa mzere uliwonse muyikepo lubani wafungo lokoma kuti pamodzi ndi bulediyo akhale wachikumbutso cha nsembe yopsereza yopereka kwa Yehova.
8 Sabata ndi sabata nthawi zonse Aaroni aziyika makeke amenewa pamaso pa Yehova mʼmalo mwa Aisraeli onse kuti akhale pangano lamuyaya.
9 Chakudyacho ndi cha Aaroni ndi ana ake ndipo azidyera ku malo wopatulika chifukwa kwa iye chakudyacho ndi chopatulika kwambiri chochokera pa chopereka chopsereza cha Yehova.”
Woyankhula Monyoza Mulungu Aphedwa ndi Miyala
10 Tsiku lina munthu wina wamwamuna amene amayi ake anali Mwisraeli koma abambo ake anali Mwigupto anapita kwa Aisraeli ndipo anakangana ndi Mwisraeli wina ku msasa.
11 Munthu uja ananyoza dzina la Yehova ndi kulitemberera. Choncho anabwera naye kwa Mose. Dzina la amayi ake linali Selomiti, mwana wa Dibiri, wa fuko la Dani.
12 Anamuyika mʼndende mpaka atadziwa bwino chofuna cha Yehova.
13 Ndipo Yehova anawuza Mose kuti,
14 “Pita naye kunja kwa msasa munthu wotembererayo. Onse amene anamumva akutemberera asanjike manja awo pamutu pake ndipo gulu lonse la anthu limugende miyala.
15 Choncho uza Aisraeli kuti, ‘Aliyense wotemberera Mulungu wake alangidwe.
16 Aliyense wonyoza dzina la Yehova, mlendo ngakhale mbadwa, aphedwe. Gulu lonse la anthu limuponye miyala.
17 “ ‘Ngati munthu wina aliyense achotsa moyo wa munthu mnzake, munthuyo ayenera kuphedwa.
18 Aliyense wopha chiweto cha mnzake ayenera kulipira china. Moyo kulipa moyo.
19 Ngati munthu avulaza mnzake, nayenso amuchite zomwe wachitira mnzakeyo:
20 kuthyola fupa kulipira kuthyola fupa, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino. Monga momwe anavulazira mnzake, amuvulaze chimodzimodzinso.
21 Aliyense wopha chiweto cha mnzake, alipire chiweto china, koma aliyense wopha munthu ayenera kuphedwa.
22 Lamulo la mlendo ndi mbadwa ndi limodzi lomweli. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”
23 Pamenepo Mose anawuza Aisraeli zimenezi, ndipo iwo anatulutsira munthu wotembererayo kunja kwa msasa ndi kumugenda miyala. Aisraeli anachita zimene Yehova analamula Mose.