20
Zilango za Tchimo
1 Yehova anawuza Mose kuti,
2 “Uza Aisraeli kuti, ‘Mwisraeli aliyense kapena mlendo aliyense wokhala mu Israeli wopereka mwana wake kwa Moleki ayenera kuphedwa. Anthu a mʼdera lakelo amuphe ndi miyala.
3 Munthu ameneyo ndidzamufulatira ndi kumuchotsa pakati pa anzake.’ Popereka mwana wake kwa Moleki, wadetsa malo anga wopatulika ndi kuyipitsa dzina langa loyera.
4 Ngati anthu a mʼderalo achita ngati sakumuona munthuyo pamene akupereka mwana wake kwa Moleki ndi kusamupha,
5 Ineyo ndidzamufulatira pamodzi ndi banja lake. Ndidzawachotsa pakati pa anthu anzawo onse amene anamutsatira, nadziyipitsa okha popembedza Moleki.”
6 “ ‘Ngati munthu adzapita kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa kapena kwa owombeza, nadziyipitsa powatsatira iwowo, Ine ndidzamufulatira ndi kumuchotsa pakati pa anthu anzake.
7 “ ‘Chifukwa chake dzipatuleni ndi kukhala woyera popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
8 Ndipo sungani malangizo anga ndi kuwatsata. Ine ndine Yehova amene ndimakuyeretsani.
9 “ ‘Munthu aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa. Magazi ake adzakhala pamutu pake chifukwa iye watemberera abambo kapena amayi ake.
10 “ ‘Ngati munthu wachita chigololo ndi mkazi wa mnzake, mwamunayo pamodzi ndi mkaziyo ayenera kuphedwa.
11 “ ‘Ngati munthu agonana ndi mkazi wa abambo ake, wachititsa manyazi abambo ake. Munthuyo pamodzi ndi mkaziyo ayenera kuphedwa. Magazi awo adzakhala pa mitu pake.
12 “ ‘Ngati munthu agonana ndi mkazi wa mwana wake, awiriwo ayenera kuphedwa. Iwo achita chinthu chonyansa kwambiri. Magazi awo adzakhala pa mitu pawo.
13 “ ‘Ngati munthu agonana ndi mwamuna mnzake ngati akugonana ndi mkazi, ndiye kuti onsewo achita chinthu cha manyazi. Choncho aphedwe. Magazi awo adzakhala pa mitu pawo.
14 “ ‘Ngati munthu akwatira mkazi, nakwatiranso amayi ake, chimenecho ndi chinthu choyipa kwambiri. Mwamunayo pamodzi ndi akaziwo ayenera kutenthedwa pa moto kuti chinthu choyipa chotere chisapezekenso pakati panu.
15 “ ‘Ngati mwamuna agonana ndi nyama, iye ayenera kuphedwa, ndipo muyeneranso kupha nyamayo.
16 “ ‘Ngati mkazi agonana ndi nyama, aphedwe pamodzi ndi nyamayo. Mkaziyo ndi nyamayo ayenera kuphedwa, ndipo magazi awo adzakhala pa mitu pawo.
17 “ ‘Ngati munthu akakwatira mlongo wake, mwana wamkazi wa abambo ake, kapena mwana wamkazi wa amayi ake, ndipo iwo nʼkugonana, ndiye kuti achita chinthu chochititsa manyazi. Onse awiri ayenera kuchotsedwa pa gulu la abale awo. Tsono popeza munthuyo wachititsa manyazi mlongo wake, adzayenera kulandira chilango.
18 “ ‘Ngati munthu agonana ndi mkazi pa nthawi yake yosamba, ndiye kuti wavula msambo wake, ndipo mkaziyo wadzivulanso. Onse awiri achotsedwe pakati pa anthu anzawo.
19 “ ‘Musagonane ndi mchemwali wa amayi anu kapena abambo anu, pakuti kutero ndi kuchititsa manyazi mʼbale wanu. Nonse mudzalipira mlandu wanu.
20 “ ‘Ngati munthu agonana ndi azakhali ake, munthuyo wachititsa manyazi a malume ake. Onse adzalipira mlandu wawo. Onsewo adzafa wopanda mwana.
21 “ ‘Munthu akakwatira mkazi wa mchimwene wake ndiye kuti wachita chinthu chonyansa. Wachititsa manyazi mʼbale wakeyo. Onse awiriwo adzakhala wopanda mwana.
22 “ ‘Nʼchifukwa chake muzisunga malangizo anga onse ndi malamulo anga ndipo muwatsatire kuti ku dziko limene Ine ndikupita nanu kuti mukakhalemo lisakakusanzeni.
23 Musatsanzire miyambo ya mitundu ya anthu imene ndi kuyipirikitsa inu mukufika. Chifukwa iwo anachita zinthu zonsezi, ndipo Ine ndinanyansidwa nawo.
24 Koma Ine ndinakuwuzani kuti, ‘Mudzatenga dziko lawo. Ine ndidzakupatsani dzikolo kuti likhale cholowa chanu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.’ Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndakupatulani pakati pa mitundu yonse ya anthu.
25 “ ‘Chifukwa chake muzisiyanitsa pakati pa nyama zoyeretsedwa ndi nyama zodetsedwa ndiponso pakati pa mbalame zoyeretsedwa ndi mbalame zodetsedwa. Musadzidetse pakudya nyama iliyonse kapena mbalame, kapena chilichonse chimene chimakwawa pansi, chimene Ine ndachipatula kuti chikhale chodetsedwa kwa inu.
26 Muzikhala woyera pamaso panga chifukwa Ine Yehova, ndine woyera ndipo ndakupatulani pakati pa anthu a mitundu yonse kuti mukhale anthu anga.
27 “ ‘Mwamuna kapena mkazi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa kapena wanyanga pakati panu ayenera kuphedwa. Muwagende ndi miyala, ndipo magazi awo adzakhala pa mitu pawo.’ ”