13
Malamulo a Nthenda za pa Khungu Zopatsirana
1 Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti,
2 “Munthu akakhala ndi chithupsa, kapena mʼbuko, kapena chikanga pa thupi lake chimene chitha kusanduka nthenda ya khate, abwere naye munthuyo kwa Aaroni wansembe kapena kwa mmodzi mwa ana ake amene ndi ansembe.
3 Tsono wansembe ayangʼanitsitse nthendayo pa khungupo, ndipo ngati ubweya wa pamalo pamene pali nthendapo wasanduka woyera, komanso kuti nthendayo yazama mʼkati kupitirira khungu, ndiye kuti nthendayo ndi khate. Wansembe akamuonetsetsa alengeze kuti ndi wodetsedwa.
4 Ngati chikanga cha pa khungulo chikuoneka choyera, ndipo kuya kwake sikukuonekera kuti kwapitirira khungu ndi ubweya wake pamalopo sunasanduke woyera, wansembe amuyike wodwalayo padera kwa masiku asanu ndi awiri.
5 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe amuonenso bwino wodwalayo. Ndipo ngati waona kuti nthendayo sinasinthe ndipo sinafalikire pa khungu, amuyikenso wodwalayo padera kwa masiku ena asanu ndi awiri.
6 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembeyo amuonenso bwino munthuyo, ndipo ngati nthendayo yazima ndi kusafalikira pa khungu, wansembe amutchule munthuyo kuti ndi woyera. Umenewo unali mʼbuko chabe. Choncho munthuyo achape zovala zake ndipo adzakhala woyera.
7 Koma ngati mʼbukowo ufalikira pakhungu atakadzionetsa kale kwa wansembe ndipo wansembeyo nʼkulengeza kuti munthuyo ndi woyeretsedwa, ndiye kuti apitenso kukadzionetsa kwa wansembeyo.
8 Wansembe amuonetsetsenso munthuyo, ndipo ngati mʼbukowo wafalikira pa khungu, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa ndi kuti nthendayo ndi khate.
9 “Ngati munthu aliyense ali ndi nthenda ya pakhungu yoyipitsa thupi, wodwalayo abwere naye kwa wansembe.
10 Wansembe amuonetsetse munthuyo, ndipo ngati ali ndi chithupsa chamaonekedwe woyera pa khungupo chimene chasandutsa ubweya wa pamalopo kukhala woyera, ndipo ngati pali zilonda pa chotupacho,
11 limenelo ndi khate lachikhalire la pa khungu, ndipo wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Asamutsekere munthu woteroyo pakuti ndi wodetsedwa kale.
12 “Ndipo ngati, mʼkuona kwa wansembe, khate lija lafalikira pa khungu lonse moti lamugwira thupi lonse kuyambira kumutu mpaka kumapazi,
13 wansembe amuonetsetse munthuyo, ndipo ngati khatero lagwira thupi lake lonse, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyera. Popeza kuti thupi lonse lasanduka loyera, munthuyo ndi woyeretsedwa.
14 Koma pa tsiku limene zilonda zidzaoneka pa iye, munthuyo adzakhala wodetsedwa.
15 Wansembe aonetsetse zilondazo ndipo alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Zilondazo ndi zodetsedwa ndipo ili ndi khate.
16 Koma zilondazo zikasinthika ndi kusanduka zoyera, munthuyo ayenera kupita kwa wansembe.
17 Wansembe amuonetsetse ndipo ngati zilondazo zasanduka zoyera, wansembe amutchule wodwalayo kuti ndi woyera ndipo adzakhala woyera ndithu.
18 “Ngati pa khungu la munthu wodwalayo pali chithupsa chimene chinapola kale,
19 ndipo pamalo pamene panali chithupsacho pakatuluka chotupa choyera kapena banga loyera mofiirira, munthuyo ayenera kukadzionetsa kwa wansembe.
20 Wansembe aonetsetse bwino ndipo ngati chikuoneka kuti chazama, ndipo ubweya wa pamalopo wasanduka woyera, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate imene yatuluka mʼchithupsacho.
21 Koma ngati wansembe waonetsetsa napeza kuti palibe ubweya woyera ndipo chithupsacho sichinazame, koma chazimirira, wansembeyo amuyike padera wodwalayo kwa masiku asanu ndi awiri.
22 Ngati nthendayo ikufalikira pa khungu, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Limeneli ndi khate.
23 Koma bangalo likakhala malo amodzi, wosafalikira, chimenecho ndi chipsera cha chithupsacho, ndipo wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyera.
24 “Munthu akakhala ndi bala lamoto pa khungu lake, ndipo chilonda cha balalo chikasanduka banga loyera mofiirira kapena loyera,
25 wansembe aonetsetse bangalo, ndipo ngati ubweya wa pa bangapo usanduka woyera, ndipo balalo lioneka kuti ndi lozama, limenelo ndi khate lomwe latuluka pa balalo. Wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Limenelo ndi khate la pa khungu.
26 Koma ngati wansembe waonetsetsa balalo ndipo palibe ubweya woyera, ndipo ngati balalo silinazame ndi kuti lazirala, wansembe amuyike padera wodwalayo kwa masiku asanu ndi awiri.
27 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe amuonenso wodwalayo, ndipo ngati bangalo lafalikira pa khungu, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Limenelo ndi khate.
28 Koma ngati bangalo likhala pa malo amodzi wosafalikira pa khungu, ndipo lazimirira, limenelo ndi thuza la bala lamoto, ndipo wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyera. Chimenecho ndi chipsera chamoto.
29 “Mwamuna kapena mkazi akakhala ndi nthenda kumutu kapena ku chibwano,
30 wansembe aonetsetse balalo ndipo likaoneka kuti lazama, ndipo ubweya wa pamalopo wasanduka wachikasu ndi wonyololoka, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Zimenezo ndi mfundu zonyerenyetsa, khate lakumutu kapena ku chibwano.
31 Koma wansembe akaonetsetsa mfundu zonyerenyetsazo, ndipo zikaoneka kuti sizinazame ndi kuti palibe ubweya wakuda, wansembe amuyike padera munthuyo kwa masiku asanu ndi awiri.
32 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe aonetsetsenso mfundu zonyerenyetsazo, ndipo ngati sizinafalikire ndipo palibe ubweya wachikasu pamalopo ndiponso sizinazame,
33 wodwalayo ametedwe, koma pamene pali mfunduyo pasametedwe. Wansembe amuyike padera munthuyo kwa masiku enanso asanu ndi awiri.
34 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe aonetsetsenso mfundu zonyerenyetsazo ndipo ngati sizinafalikire pa khungu ndi kuti sizinazame, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyera. Tsono achape zovala zake, ndipo adzakhala woyera.
35 Koma mfundu zonyerenyetsazo zikafalikira pa khungu, wansembe atalengeza kuti ndi woyera,
36 wansembe amuonetsetsenso wodwalayo ndipo ngati mfunduzo zafalikira pa khungu, iye asalabadirenso zoyangʼana ngati ubweya uli wachikasu. Munthuyo ndi wodetsedwa.
37 Koma ngati wansembe waonetsetsa kuti mfunduzo sizinasinthe ndipo ubweya wakuda wamera pa mfundupo, ndiye kuti wodwalayo wachira. Tsono wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyeretsedwa.
38 “Mwamuna kapena mkazi akakhala ndi mawanga woyera pa khungu,
39 wansembe aonetsetse mawangawo, ndipo ngati ali otuwa, ndiye kuti ndi mibuko chabe yotuluka pa khungu. Munthuyo ndi woyera.
40 “Tsitsi la munthu likayoyoka kumutu ndiye kuti ndi dazi limenelo koma munthuyo ndi woyeretsedwa.
41 Ngati tsitsi lake layoyoka chapamphumi ndiye kuti ndi dazi la pa chipumi limenelo koma munthuyo ndi woyera.
42 Koma ngati pa dazi la pamutu kapena la pa chipumi pakhala chithupsa choyera mofiirira, ndiye kuti ndi khate limenelo lochokera mu dazi la pamutu lija kapena pa chipumi lija.
43 Tsono wansembe amuonetsetse wodwalayo ndipo ngati chithupsa cha pa dazi lapankhongo kapena pa dazi lapachipumicho ndi choyera mofiirira monga nthenda ya khate imaonekera,
44 ndiye kuti munthuyo ali ndi khate, motero ndi wodetsedwa. Wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa chifukwa cha chithupsa cha pamutu pakepo.
45 “Munthu wa khate lotere avale sanza, tsitsi lake alilekerere, aphimbe mlomo wake wapamwamba ndipo azifuwula kuti, ‘Ndine wodetsedwa, ndine wodetsedwa!’
46 Munthu wodwalayo adzakhala wodetsedwa kwa nthawi yonse imene ali ndi nthendayo. Iye ayenera kumakhala payekha kunja kwa msasa.
Malamulo a Nguwi ya pa Zovala
47 “Nsalu iliyonse ikakhala ndi nguwi,
48 kaya ndi chovala chopangidwa ndi nsalu yathonje kapena yaubweya, yoluka ndi thonje kapena ubweya, yachikopa kapena yopangidwa ndi chikopa,
49 ndipo ngati pamalo pamene pachita nguwiyo pali ndi maonekedwe obiriwira kapena ofiirira imeneyo ndi nguwi yoyipitsa chovala ndipo chovalacho chikaonetsedwe kwa wansembe.
50 Wansembeyo ayionetsetse nguwiyo ndipo chovalacho achiyike padera kwa masiku asanu ndi awiri.
51 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri ayionetsetsenso nguwiyo ndipo ngati nguwiyo yafalikira pa chovalacho, chathonje kapena chaubweya, kapena pa chikopacho, kaya ndi cha ntchito ya mtundu wanji, imeneyo ndi nguwi yoopsa ndipo chovalacho ndi chodetsedwa.
52 Wansembe atenthe chovala chathonje kapena chaubweya chija, ngakhalenso chinthu chachikopa chija popeza nguwiyo yachidetsa. Nguwiyo ndi yoopsa choncho chinthucho achitenthe.
53 “Koma ngati wansembe akayangʼanitsitsa nguwiyo apeza kuti sinafalikire pa chovalacho kapena pa chinthu chilichonse chachikopa,
54 iye alamulire kuti chinthu choyipitsidwacho achichape. Akatero achiyike padera kwa masiku enanso asanu ndi awiri.
55 Chovalacho chitachapidwa, wansembe achionenso ndipo ngati nguwiyo sinasinthe maonekedwe ake, ngakhale kuti sinafalikire, chovalacho ndi chodetsedwa ndithu. Muchitenthe, ngakhale kuti nguwiyo ili kumbuyo kapena kumaso kwa chinthucho.
56 Koma ngati wansembe aonetsetsa nʼkupeza kuti nguwi ija yathimbirira pa chovala chija kapena pa chinthu chachikopa chija atachichapa, ndiye angʼambeko chinthucho pa banga la nguwiyo.
57 Koma ngati nguwiyo iwonekanso pa chovala chathonje kapena chaubweya ndiye kuti nguwiyo ikufalikira. Chilichonse chimene chili ndi nguwi chiyenera kutenthedwa.
58 Chovala chathonje kapena chaubweya, ngakhale chinthu china chilichonse chopangidwa ndi chikopa, mukachichapa nguwi yake nʼkuchoka muchichapenso kawiri ndipo chidzakhala choyeretsedwa.”
59 Amenewa ndiwo malamulo a nguwi yokhala pa chovala chaubweya kapena pa chovala chathonje, kapenanso pa chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa kuti muzitha kulekanitsa choyeretsedwa ndi chodetsedwa.