Maliro   
1
1 Haa! Mzinda uja wasiyidwa wokhawokha,  
umene kale unali wodzaza ndi anthu!  
Kale unali wotchuka pakati pa mitundu ya anthu!  
Tsopano wasanduka ngati mkazi wamasiye.  
Kale unali mfumukazi ya onse pa dziko lapansi,  
tsopano wasanduka kapolo.   
   
 
2 Ukulira mowawidwa mtima usiku wonse,  
misozi ili pa masaya pake.  
Mwa abwenzi ake onse,  
palibe ndi mmodzi yemwe womutonthoza.  
Abwenzi ake onse amuchitira chiwembu;  
onse akhala adani ake.   
   
 
3 Yuda watengedwa ku ukapolo,  
kukazunzika ndi kukagwira ntchito yolemetsa.  
Iye akukhala pakati pa anthu a mitundu ina;  
ndipo alibe malo opumulira.  
Onse omuthamangitsa iye amupitirira,  
ndipo alibe kwina kothawira.   
   
 
4 Misewu yopita ku Ziyoni ikulira,  
chifukwa palibe ndi mmodzi yemwe akubwera ku maphwando ake.  
Zipata zake zonse zili pululu,  
ansembe akubuwula.  
Anamwali ake akulira,  
ndipo ali mʼmasautso woopsa.   
   
 
5 Adani ake asanduka mabwana ake;  
odana naye akupeza bwino.  
Yehova wamubweretsera mavuto  
chifukwa cha machimo ake ambiri.  
Ana ake atengedwa ukapolo  
pamaso pa mdani.   
   
 
6 Ulemerero wonse wa mwana wamkazi wa Ziyoni  
wachokeratu.  
Akalonga ake ali ngati mbawala  
zosowa msipu;  
alibe mphamvu zothawira  
owathamangitsa.   
   
 
7 Pa masiku a masautso ndi kuzunzika kwake,  
Yerusalemu amakumbukira chuma chonse  
chimene mʼmasiku amakedzana chinali chake.  
Anthu ake atagwidwa ndi adani ake,  
panalibe aliyense womuthandiza.  
Adani ake ankamuyangʼana  
ndi kumuseka chifukwa cha kuwonongeka kwake.   
   
 
8 Yerusalemu wachimwa kwambiri  
ndipo potero wakhala wodetsedwa.  
Onse amene ankamulemekeza pano akumunyoza,  
chifukwa aona umaliseche wake.  
Iye mwini akubuwula  
ndipo akubisa nkhope yake.   
   
 
9 Uve wake umaonekera pa zovala zake;  
iye sanaganizire za tsogolo lake.  
Nʼchifukwa chake kugwa kwake kunali kwakukulu;  
ndipo analibe womutonthoza.  
“Inu Yehova, taonani masautso anga,  
pakuti mdani wapambana.”   
   
 
10 Adani amulanda  
chuma chake chonse;  
iye anaona mitundu ya anthu achikunja ikulowa mʼmalo ake opatulika,  
amene Inu Mulungu munawaletsa  
kulowa mu msonkhano wanu.   
   
 
11 Anthu ake onse akubuwula  
pamene akufunafuna chakudya;  
asinthanitsa chuma chawo ndi chakudya  
kuti akhale ndi moyo.  
“Inu Yehova, taonani ndipo ganizirani,  
chifukwa ine ndanyozeka.”   
   
 
12 “Kodi zimenezi mukuziyesa zachabe, inu nonse mukudutsa?  
Yangʼanani ndipo muone.  
Kodi pali mavuto ofanana ndi  
amene andigwerawa,  
amene Ambuye anandibweretsera  
pa tsiku la ukali wake?   
   
 
13 “Anatumiza moto kuchokera kumwamba,  
unalowa mpaka mʼmafupa anga.  
Anayala ukonde kuti ukole mapazi anga  
ndipo anandibweza.  
Anandisiya wopanda chilichonse,  
wolefuka tsiku lonse.   
   
 
14 “Wazindikira machimo anga onse  
ndipo ndi manja ake anawaluka pamodzi.  
Machimowa afika pakhosi panga,  
ndipo Ambuye wandithetsa mphamvu.  
Iye wandipereka  
kwa anthu amene sindingalimbane nawo.   
   
 
15 “Ambuye wakana  
anthu anga onse amphamvu omwe ankakhala nane:  
wasonkhanitsa gulu lankhondo kuti lilimbane nane,  
kuti litekedze anyamata anga;  
mʼmalo ofinyira mphesa Ambuye wapondereza  
anamwali a Yuda.   
   
 
16 “Chifukwa cha zimenezi ndikulira  
ndipo maso anga adzaza ndi misozi.  
Palibe aliyense pafupi woti anditonthoze,  
palibe aliyense wondilimbitsa mtima.  
Ana anga ali okhaokha  
chifukwa mdani watigonjetsa.   
   
 
17 “Ziyoni wakweza manja ake,  
koma palibe aliyense womutonthoza.  
Yehova walamula kuti abale ake  
a Yakobo akhale adani ake;  
Yerusalemu wasanduka  
chinthu chodetsedwa pakati pawo.   
   
 
18 “Yehova ndi wolungama,  
koma ndine ndinawukira malamulo ake.  
Imvani inu anthu a mitundu yonse;  
onani masautso anga.  
Anyamata ndi anamwali anga  
agwidwa ukapolo.   
   
 
19 “Ndinayitana abwenzi anga  
koma anandinyenga.  
Ansembe ndi akuluakulu anga  
anafa mu mzinda  
pamene ankafunafuna chakudya  
kuti akhale ndi moyo.   
   
 
20 “Inu Yehova, onani mmene ine ndavutikira!  
Ndikuzunzika mʼkati mwanga,  
ndipo mu mtima mwanga ndasautsidwa  
chifukwa ndakhala osamvera.  
Mʼmisewu anthu akuphedwa,  
ndipo ku mudzi kuli imfa yokhayokha.   
   
 
21 “Anthu amva kubuwula kwanga,  
koma palibe wonditonthoza.  
Adani anga onse amva masautso anga;  
iwo akusangalala pa zimene Inu mwachita.  
Lifikitseni tsiku limene munalonjeza lija  
kuti iwonso adzakhale ngati ine.   
   
 
22 “Lolani kuti ntchito zawo zoyipa zifike pamaso panu;  
muwalange  
ngati mmene mwandilangira ine  
chifukwa cha machimo anga onse.  
Ndikubuwula kwambiri  
ndipo mtima wanga walefuka.”