5
Naamani Achiritsidwa Khate Lake
1 Tsono Naamani anali mtsogoleri wa gulu lankhondo a mfumu ya ku Aramu. Iye anali munthu wodalirika pamaso pa mbuye wake ndipo anali wokondedwa kwambiri, chifukwa kudzera mwa iye Yehova anapambanitsa Aaramu. Anali msilikali wolimba mtima, koma anali ndi khate.
2 Tsono magulu a Aaramu anapita ku nkhondo ndipo anakagwira ukapolo mtsikana wamngʼono wa ku Israeli, ndipo ankatumikira mkazi wa Naamani.
3 Mtsikanayo anawuza mkazi wa Naamani kuti, “Mbuye wanga akanapita kukaonana ndi mneneri amene amakhala ku Samariya, akanachiritsidwa khate lawo.”
4 Naamani anapita kwa mbuye wake kukamuwuza zomwe mtsikana wochokera ku Israeli ananena.
5 Mfumu ya ku Aramu inayankha kuti, “Iwe uyenera kupita. Ine ndilembera kalata mfumu ya ku Israeli.” Choncho Naamani ananyamuka kupita ku Samariya, atatenga ndalama za siliva 30,000, ndalama zagolide 6,000 ndiponso zovala khumi za pa chikondwerero.
6 Kalata imene anapita nayo kwa mfumu ya ku Israeli inali ndi mawu awa: “Taonani, ndikutumiza Naamani mtumiki wanga pamodzi ndi kalatayi kwa inu kuti mumuchiritse khate lake.”
7 Mfumu ya ku Israeli itangowerenga kalatayo, inangʼamba mkanjo wake ndipo inati, “Kodi ine ndine Mulungu? Kodi ndingathe kupha kapena kupereka moyo? Chifukwa chiyani munthu ameneyu wanditumizira munthu woti ndimuchiritse khate lake? Taonani, iyeyu akungofuna kuti apeze chifukwa choyambanirana nane!”
8 Elisa munthu wa Mulungu atamva kuti mfumu ya ku Israeli yangʼamba mkanjo wake, anatumiza uthenga uwu: “Chifukwa chiyani mwangʼamba mkanjo wanu? Mutumizeni munthuyo kwa ine ndipo iyeyo adzadziwa kuti muli mneneri mu Israeli.”
9 Choncho Naamani anapita pamodzi ndi akavalo ake ndi magaleta nakayima pa khomo la nyumba ya Elisa.
10 Elisa anatumiza uthenga kwa iye woti, “Pita, kasambe kasanu ndi kawiri mu mtsinje wa Yorodani, thupi lako lidzachira ndi kukhalanso monga kale ndipo udzayeretsedwa.”
11 Koma Naamani anachoka mokwiya ndipo anati, “Ine ndimaganiza kuti munthuyu atuluka ndipo ayimirira nayitana dzina la Yehova Mulungu wake, nayendetsa dzanja lake pamwamba pa nthendayi ndi kundichiritsa khate langa.
12 Kodi Abana ndi Faripara, mitsinje ya ku Damasiko, siyoposa mitsinje ina yonse ya ku Israeli? Kodi sindikanasamba mʼmitsinje imeneyo ndi kuyeretsedwa?” Kotero anatembenuka nachoka ali wokwiya kwambiri.
13 Antchito ake anamuyandikira namufunsa kuti, “Abambo anga, mneneri akanakulamulani chinthu chachikulu, kodi inu simukanachita? Nanga nʼzovuta motani zomwe mneneri wanena kuti ‘Kasambeni ndipo mudzayeretsedwa!’ ”
14 Choncho Naamani anapita ku Yorodani nakadzimiza mʼmadzimo kasanu nʼkawiri, monga momwe munthu wa Mulungu anamuwuzira. Thupi lake linakhalanso monga kale ndipo linakhala losalala ngati la kamnyamata.
15 Pamenepo Naamani ndi atumiki ake onse anabwerera kwa munthu wa Mulungu uja. Naamani anayima pamaso pa Elisa ndipo anati, “Tsopano ndikudziwa kuti kulibe Mulungu wina pa dziko lonse lapansi koma mu Israeli mokha. Chonde, tsopano landirani mphatso ya mtumiki wanu.”
16 Mneneri anayankha kuti, “Pali Yehova wamoyo, amene ine ndimamutumikira, sindidzalandira zimenezi.” Ndipo ngakhale Naamani anamukakamiza, iye anakanabe.
17 Naamani anati, “Ngati inu simulandira, chonde lolani mtumiki wanu kuti atengeko dothi lokwanira kunyamula abulu awiri, popeza mtumiki wanu sadzaperekanso nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa mulungu wina koma Yehova.
18 Koma Yehova andikhululukire ine pa chinthu ichi: Pamene mbuye wanga alowa mʼnyumba ya mapemphero ya Rimoni ine ndimapita naye ndipo ndimakagwada naye limodzi. Pamene ndikugwada mʼnyumba ya mapemphero ya Rimoni, Yehova azikhululukira mtumiki wanu pa chinthu chimenechi.”
19 Elisa anati, “Pita mu mtendere.”
Choncho anachoka nayenda pangʼono.
20 Koma Gehazi, mtumiki wa Elisa munthu wa Mulungu, anaganiza mu mtima mwake kuti, “Taonani, mbuye wanga wamulekerera Naamani Mwaramuyu, posalandira zomwe anabweretsa. Pali Yehova wamoyo, ine ndimuthamangira ndipo ndikatengako zinthu kwa iye.”
21 Choncho Gehazi anamuthamangira Naamani uja. Naamani ataona Gehazi akumuthamangira, anatsika mʼgaleta lake ndi kukakumana naye. Iye anafunsa Gehazi kuti, “Kodi nʼkwabwino?”
22 Gehazi anayankha kuti, “Inde nʼkwabwino. Mbuye wanga wandituma kuti ndidzakuwuzeni kuti, ‘Anyamata awiri mwa ana a aneneri angondipeza kumene kuchokera ku dziko la mapiri la Efereimu. Chonde apatseniko ndalama za siliva 3,000 ndi zovala ziwiri za pa phwando.’ ”
23 Naamani anati, “Kuli bwino utenge ndalama zasiliva 6,000.” Iye anakakamiza Gehazi kuti alandire, ndipo kenaka anamanga matumba awiri a ndalama zasiliva pamodzi ndi zovala zinayi za pa mphwando. Naamani anazipereka kwa antchito ake awiri ndipo anazinyamula nayenda patsogolo pa Gehazi.
24 Gehazi atafika ku phiri, anawalanda antchito aja zinthu zija nazibisa mʼnyumbamo. Iye anawawuza anthu aja kuti abwerere ndipo anapita.
25 Kenaka analowa mʼnyumbamo nakayima pamaso pa mbuye wake Elisa.
Elisa anafunsa kuti, “Kodi Gehazi unali kuti?”
Iye anayankha kuti, “Mtumiki wanu sanapite kwina kulikonse.”
26 Koma Elisa anati kwa Gehazi, “Kodi mzimu wanga sunali nawe pamene munthu uja anatsika mʼgaleta lake ndi kukumana nawe? Kodi ino ndi nthawi yolandira ndalama, kapena kulandira zovala, mitengo ya olivi, minda ya mpesa, nkhosa, ngʼombe kapena antchito aamuna kapena antchito aakazi?
27 Khate la Naamani lidzakumatirira iwe ndi zidzukulu zako mpaka muyaya.” Ndipo Gehazi anachoka pamaso pa Elisa ali ndi khate lotuwa ngati phulusa.