13
Yehowahazi Mfumu ya Israeli
1 Mʼchaka cha 23 cha ufumu wa Yowasi mwana wa Ahaziya mfumu ya Yuda, Yehowahazi, mwana wa Yehu anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya, ndipo analamulira zaka 17.
2 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova potsatira machimo a Yeroboamu mwana Nebati amene anachimwitsa nawo Israeli ndipo iye sanawaleke machimowo.
3 Ndipo Yehova anakwiyira Aisraeli nawayika pansi pa ulamuliro wa Hazaeli mfumu ya Siriya ndi Beni-Hadadi mwana wa Hazaeli masiku awo onse.
4 Tsono Yehowahazi anapempha Yehova kuti amuchitire chifundo ndipo Yehova anamva pempho lake chifukwa anaona momwe mfumu ya Aramu inkapsinjira Aisraeli.
5 Yehova anapatsa Aisraeli munthu woti awapulumutse ndipo anapulumuka mʼdzanja la Aramu. Choncho Aisraeli anakhala mʼnyumba zawo monga ankachitira kale.
6 Komabe Aisraeli sanaleke kuchita machimo a nyumba ya Yeroboamu, amene anachimwitsa nawo Israeli. Iwo anapitirira kuchita machimowo. Ndiponso fano la Asera linakhalabe ku Samariya.
7 Yehowahazi sanatsale ndi ankhondo ambiri koma 50 okha okwera pa akavalo, magaleta khumi ndi asilikali oyenda pansi 10,000.
8 Ntchito zina za Yehowahazi ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli?
9 Yehowahazi anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu Samariya. Ndipo Yowasi mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Yehowasi Mfumu ya Israeli
10 Mʼchaka cha 37 cha Yowasi mfumu ya Yuda, Yehowahazi anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya, ndipo analamulira zaka 16.
11 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova ndipo sanaleke kuchita tchimo la Yeroboamu mwana wa Nebati limene anachimwitsa nalo Israeli.
12 Ntchito zina za Yowasi ndi zonse zimene anachita, kuphatikizapo nkhondo yake ndi Amaziya mfumu ya Yuda, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli?
13 Yowasi anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake ndipo Yeroboamu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. Yowasi anayikidwa mʼmanda mu Samariya pamodzi ndi mafumu a Israeli.
14 Tsono Elisa anadwala matenda amene anafa nawo. Yowasi mfumu ya Israeli inapita kukamuona ndipo inamulirira. Iye polira ankanena kuti, “Abambo anga! Abambo anga! Magaleta a Israeli ndi okwerapo ake a Israeli!”
15 Elisa anamuwuza kuti, “Tenga uta ndi mivi.” Ndipo anaterodi.
16 Elisa anawuza mfumu ya Israeli kuti, “Tenga uta mʼdzanja lako.” Pamene anatenga utawo, Elisa anayika manja ake pa manja a mfumuyo.
17 Elisa anamuwuza kuti, “Tsekula zenera.” Ndipo anatsekuladi. Elisa anati, “Ponya muviwo!” Ndipo anaponyadi. Elisa anati, “Muvi wa chigonjetso cha Yehova, muvi wogonjetsera Aaramu! Iwe udzawawononga kwathunthu Aaramu ku Afeki.”
18 Kenaka Elisa anati, “Tenga mivi.” Ndipo mfumu inatenga miviyo. Iye anati, “Lasa pansi.” Mfumu inalasa pansi miviyo katatu nʼkuleka.
19 Munthu wa Mulungu anapsera mtima mfumuyo ndipo anati, “Ukanalasa pansi kasanu kapena kasanu nʼkamodzi. Pamenepo ukanatha kuwagonjetsa Aaramu ndi kuwawononga kwathunthu. Koma tsopano udzawagonjetsa katatu kokha.”
20 Elisa anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda.
Tsono magulu a ankhondo a Amowabu ankabwera kudzalowa ndi kudzathira nkhondo dzikolo nthawi ya dzinja.
21 Tsiku lina Aisraeli ena akukayika maliro mʼmanda, mwadzidzidzi anaona gulu lankhondo ndipo munthu womwalirayo anamuponyera mʼmanda a Elisa. Pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, munthu wakufayo anatsitsimuka nayimirira.
22 Hazaeli mfumu ya Aramu inazunza Aisraeli nthawi yonse ya ulamuliro wa Yehowahazi.
23 Koma Yehova anawachitira chifundo Aisraeliwo ndi kukhudzika ndi zomwe zinkawachitikira chifukwa cha pangano lake ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Mpaka lero lino Iye sanafune kuwawononga kapena kuwachotsa pamaso pake.
24 Hazaeli mfumu ya Aramu inamwalira ndipo mwana wake Beni-Hadadi analowa ufumu mʼmalo mwake.
25 Pamenepo Yowasi mwana wa Yehowahazi analandanso kwa Beni-Hadadi mwana wa Hazaeli mizinda yonse imene iye analanda Yehowahazi abambo ake. Yehowasi anagonjetsa Beni-Hadadi katatu ndipo anatenganso mizinda ya Israeli.