5
Kukonzekera Kumanga Nyumba ya Mulungu
1 Hiramu mfumu ya ku Turo atamva kuti Solomoni wadzozedwa kukhala mfumu mʼmalo mwa abambo ake Davide, anatumiza akazembe ake kwa Solomoni, chifukwa mfumu Hiramu inali pa ubale wabwino ndi Davide nthawi zonse.
2 Solomoni anabweza mawu awa kwa Hiramu:
3 “Inu mukudziwa kuti chifukwa cha nkhondo zimene zinkachokera ku mbali zonse kulimbana ndi abambo anga, iwo sanathe kumangira Nyumba Yehova Mulungu wawo, mpaka Yehova atawayika adani awo pansi pa ulamuliro wawo.
4 Koma tsopano Yehova Mulungu wanga wandipatsa mtendere mbali zonse za dziko ndipo ndilibe mdani kapena chovuta chilichonse.
5 Choncho ine ndikufuna kumangira nyumba Yehova Mulungu wanga, monga momwe Iye anawuzira abambo anga Davide kuti, ‘Mwana wako amene ndidzamukhazike pa mpando waufumu mʼmalo mwako ndiye adzandimangire Nyumba.’
6 “Choncho lamulani kuti andidulire mikungudza ya ku Lebanoni. Anthu anga adzagwira ntchito imeneyo pamodzi ndi anthu anuwo, ndipo ine ndidzalipira anthu anuwo malipiro amene inu mungakhazikitse. Inu mukudziwa kuti ife tilibe anthu aluso locheka matabwa monga Asidoni.”
7 Hiramu anakondwa kwambiri atamva uthenga wa Solomoni ndipo anati, “Lero Yehova atamandike chifukwa wapatsa Davide mwana wanzeru kuti alamulire mtundu waukuluwu.”
8 Tsono Hiramu anabweza mawu awa kwa Solomoni:
“Ndalandira uthenga umene mwanditumizira ndipo ine ndidzachita zonse zimene mukufuna pokupatsani mitengo ya mkungudza ndi payini.
9 Anthu anga adzatsika nayo kuchokera ku Lebanoni mpaka ku nyanja, ndipo adzayiyandamitsa pa nyanja mpaka ku malo amene munene. Kumeneko ndidzayimasula ndipo mudzayitenga. Ndipo inu mudzakwaniritsa chokhumba changa pondipatsa chakudya cha banja langa laufumu.”
10 Motero Hiramu anapereka kwa Solomoni mitengo yonse ya mkungudza ndi payini imene ankayifuna,
11 ndipo Solomoni anamupatsa Hiramu mitanga ya tirigu 20,000 ngati chakudya cha pa nyumba yake, kuwonjezera pa migolo ya mafuta a olivi yokwana 20,000. Solomoni anapitiriza kupereka zimenezi chaka ndi chaka.
12 Yehova anamupatsa Solomoni nzeru monga momwe analonjezera. Panali ubale wa mtendere pakati pa Solomoni ndi Hiramu, ndipo awiriwa anachita pangano.
13 Mfumu Solomoni inasonkhanitsa anthu ogwira ntchito ya thangata mʼdziko lonse la Israeli ndipo anthu athangatawo analipo 30,000.
14 Iye ankatumiza anthu 10,000 ku Lebanoni pa mwezi mosinthanasinthana, kotero kuti ankakhala ku Lebanoniko mwezi umodzi ndipo kwawo ankakhalako miyezi iwiri. Adoniramu ndiye ankayangʼanira ogwira ntchito yathangatayo.
15 Solomoni anali ndi anthu amtengatenga 70,000, anthu 80,000 osema miyala ku mapiri,
16 ndi akapitawo 33,000 amene ankayangʼanira ntchitoyi ndiponso anthu ogwira ntchito zina.
17 Molamulidwa ndi mfumu, anakumba ndi kusema miyala ikuluikulu kwambiri yoti akamangire maziko a Nyumba ya Mulungu.
18 Amisiri a Solomoni ndi a Hiramu ndiponso anthu a ku Gebala anasema miyala ndi kukonza matabwa ndi miyala yomangira Nyumba ya Mulungu.