9
Yesu Achiritsa Munthu Wosaona Chibadwire
Iye akuyendabe, anaona munthu wosaona chibadwire. Ophunzira ake anamufunsa Iye kuti, “Rabi anachimwa ndani, munthuyu kapena makolo ake, kuti iye abadwe wosaona?”
Yesu anayankha kuti, “Sikuti iyeyu anachimwa kapena makolo ake, koma izi zinachitika kuti Mulungu aonetse ntchito zake mwa iyeyu. Ife tiyenera kugwira ntchito za Iye amene anandituma kukanali masana. Usiku ukubwera, pamene wina aliyense sadzagwira ntchito. Pamene Ine ndili mʼdziko lapansi, Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi.”
Atanena izi, Iye anathira malovu pansi ndi kukanda dothi, napaka matopewo mʼmaso a munthuyo. Yesu anamuwuza iye kuti, “Pita kasambe mʼdziwe la Siloamu” (mawu awa akutanthauza Wotumidwa). Choncho munthuyo anapita ndi kukasamba ndipo anabwerako akupenya.
Anzake ndi iwo amene anamuona iye poyamba akupempha anafunsa kuti, “Kodi uyu si munthu amene amapemphapempha uja?” Ena ananena kuti anali yemweyo.
Ena anati, “Ayi, sakuoneka ngati yemweyo.”
Koma iye mwini ananenetsa kuti, “Munthuyo ndine.”
10 Iwo anafunsitsa kuti, “Kodi nanga maso ako anatsekuka bwanji?”
11 Iye anayankha kuti, “Munthu wina wotchedwa Yesu anakanda dothi ndi kupaka mʼmaso anga. Iye anandiwuza kuti ndipite ku Siloamu ndi kukasamba. Choncho ndinapita kukasamba, ndipo ndikuona.”
12 Iwo anamufunsa iye kuti, “Ali kuti munthu ameneyu?”
Iye anati, “Ine sindikudziwa.”
Afarisi Afufuza za Kuchiritsidwa Kwake
13 Iwo anabwera naye munthu amene poyamba anali wosaona kwa Afarisi. 14 Tsono linali la Sabata tsiku limene Yesu anakanda dothi ndi kutsekula maso a munthuyu. 15 Choncho Afarisi anamufunsanso iye momwe analandirira kuona kwake. Munthuyo anayankha kuti, “Iye anapaka matope mʼmaso anga, ndipo ine ndinakasamba, ndipo ndikuona.”
16 Ena a Afarisi anati, “Munthu uyu siwochokera kwa Mulungu, pakuti sasunga Sabata.”
Koma enanso anafunsa kuti, “Kodi munthu wochimwa angachite bwanji zizindikiro zodabwitsa ngati izi?” Choncho iwo anagawanika.
17 Pomaliza iwo anatembenukiranso kwa munthu amene anali wosaona uja nati, “Kodi iwe unena chiyani za Iye poti ndi maso ako amene watsekula?”
Munthuyo anayankha kuti, “Iye ndi mneneri.”
18 Ayuda sanakhulupirirebe kuti iye anali wosaona ndi kuti anayamba kuona kufikira atayitana makolo ake. 19 Iwo anafunsa kuti, “Kodi uyu ndi mwana wanu? Kodi iyeyu ndi amene mukunena kuti anabadwa wosaona? Nanga zikutheka bwanji kuti akuona?”
20 Makolo anayankha kuti, “Ife tikudziwa kuti ndi mwana wathu, ndipo tikudziwa kuti anabadwa wosaona. 21 Koma sitidziwa zimene zachitika kuti tsopano azipenya. Amenenso wamupenyetsa sitikumudziwa. Mufunseni ndi wamkulu; iye adziyankhira yekha.” 22 Makolo ake ananena izi chifukwa amaopa Ayuda, popeza Ayuda anatsimikiza kale kuti aliyense amene adzamuvomereza Yesu kuti anali Khristu adzatulutsidwa mʼsunagoge. 23 Ichi ndi chifukwa chake makolo ake anati, “Mufunseni iye ndi wamkulu.”
24 Iwo anamuyitanitsa kachiwiri munthu amene anali wosaonayo. Iwo anati, “Lemekeza Mulungu. Ife tikudziwa kuti munthu uyu ndi wochimwa.”
25 Iye anayankha kuti, “Zakuti Iye ndi wochimwa kapena ayi, ine sindikudziwa. Ine ndikudziwa chinthu chimodzi. Ndinali wosaona koma tsopano ndikuona!”
26 Kenaka anamufunsa kuti, “Kodi Iye anachita chiyani kwa iwe? Iye anatsekula motani maso ako?”
27 Iye anayankha kuti, “Ine ndakuwuzani kale ndipo inu simunamvetsetse. Chifukwa chiyani mukufuna mumvenso? Mukufuna kuti inu mukhale ophunzira akenso?”
28 Pamenepo anamunyoza ndipo anati, “Iwe ndiye ophunzira wa munthuyu! Ife ndife ophunzira a Mose! 29 Ife tikudziwa kuti Mulungu anayankhula kwa Mose, koma za munthu uyu, ife sitikudziwa ngakhale kumene akuchokera.”
30 Munthuyo anayankha kuti, “Tsopano izi ndi zodabwitsa! Inu simukudziwa kumene akuchokera, komabe iye watsekula maso anga. 31 Ife tikudziwa kuti Mulungu samvera wochimwa. Iye amamvera munthu woopa Mulungu amene amachita chifuniro chake. 32 Palibe amene anamvapo za kutsekula maso a munthu wobadwa wosaona. 33 Ngati munthu uyu akanakhala wosachokera kwa Mulungu, palibe chimene Iye akanachita.”
34 Pamenepo anayankha kuti, “Iwe unabadwa mu uchimo kotheratu; bwanji ukuyesa kutiphunzitsa ife!” Ndipo anamutulutsa kunja.
Kusaona kwa Uzimu
35 Yesu anamva kuti anamutulutsa kunja ndipo pamene anamupeza anati, “Kodi ukukhulupirira Mwana wa Munthu?”
36 Munthuyo anafunsa kuti, “Kodi, Ambuye, ameneyo ndi ndani? Ndiwuzeni kuti ndimukhulupirire Iye?”
37 Yesu anati, “Iwe wamuona tsopano. Zoonadi ndiye amene akuyankhula nawe.”
38 Pamenepo munthuyo anati, “Ambuye, ndikukhulupirira,” ndipo anamulambira Iye.
39 Yesu anati, “Ndinabwera pansi pano kudzaweruza kuti osaona aone ndi openya asaone.”
40 Afarisi ena amene anali pafupi naye anamva akunena izi ndipo anafunsa kuti, “Chiyani? Kodi ndife osaonanso?”
41 Yesu anati, “Mukanakhala osaona, simukanachimwa; koma tsopano popeza mukuti mumaona, ndinu ochimwabe.”