2
Pemphero la Yona 
 
1 Yona ali mʼmimba mwa chinsomba chija anapemphera kwa Yehova Mulungu wake.  
2 Iye anati:  
“Pamene ndinali mʼmavuto anga ndinayitana Yehova,  
ndipo Iye anandiyankha.  
Ndili ku dziko la anthu akufa ndinapempha thandizo,  
ndipo Inu munamva kulira kwanga.   
3 Munandiponya mʼnyanja yozama,  
mʼkati mwenimweni mwa nyanja,  
ndipo madzi oyenda anandizungulira;  
mafunde anu onse ndi mkokomo wake  
zinandimiza.   
4 Ndinati, ‘Ine ndachotsedwa  
pamaso panu;  
komabe ndidzayangʼananso  
ku Nyumba yanu yopatulika.’   
5 Madzi wondimiza anandichititsa mantha,  
nyanja yozama inandizungulira;  
udzu wa mʼmadzi zinakuta mutu wanga.   
6 Ndinatsikira kunsi ndithu, mʼtsinde mwa mapiri;  
mipiringidzo ya dziko inanditsekereza kosatha.  
Koma Inu munatulutsa moyo wanga mʼmandamo,  
Inu Yehova Mulungu wanga.   
   
 
7 “Pamene moyo wanga umachoka mwa ine,  
ine ndinakumbukira Inu Yehova,  
ndipo pemphero langa linafika kwa inu,  
ku Nyumba yanu yopatulika.   
   
 
8 “Iwo amene amagwiritsitsa mafano achabechabe  
amataya chisomo chawo.   
9 Koma ine ndidzapereka kwa Inu nsembe  
ndikuyimba nyimbo yamayamiko.  
Chimene ndinalonjeza ndidzachikwaniritsa.  
Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.”   
10 Ndipo Yehova analamula chinsomba chija, ndipo chinakamusanza Yonayo mʼmbali mwa nyanja.