32
Mawu a Elihu 
 
1 Tsono anthu atatuwa analeka kumuyankha Yobu, chifukwa chakuti iyeyo ankadziona kuti ndi wolungama.  
2 Koma Elihu, mwana wa Barakeli, wa fuko la Buzi, wa banja la Ramu, anapsera mtima kwambiri Yobu chifukwa choti Yobuyo anakana kuvomera kuti anachimwa ndi kuti Mulungu anakhoza pomulanga.  
3 Anapseranso mtima abwenzi ake atatu aja chifukwa sanapeze njira yomutsutsira Yobu, ngakhale iwo anamupeza kuti anali wolakwa.  
4 Tsono Elihu anadikira kuti ayankhule ndi Yobu chifukwa choti abwenziwo anali akuluakulu kupambana iyeyo.  
5 Koma Elihu ataona kuti anthu atatuwo analibe mawu oti ayankhulenso, iye anapsa mtima.   
6 Choncho Elihu mwana wa Barakeli wa fuko la Buzi anati:  
“Ine ndine wamngʼono,  
inuyo ndinu akuluakulu,  
nʼchifukwa chake ndimaopa,  
ndimachita mantha kuti ndikuwuzeni zimene ndimadziwa.   
7 Ndimaganiza kuti, ‘Ayambe ndi akuluakulu kuyankhula;  
anthu amvulazakale ndiwo amaphunzitsa nzeru.’   
8 Koma mzimu wa Mulungu mwa munthu,  
mpweya wa Wamphamvuzonse, ndi umene umapereka nzeru zomvetsa zinthu.   
9 Si okalamba amene ali ndi nzeru,  
si amvulazakale okha amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu zimene zili zoyenera.   
   
 
10 “Nʼchifukwa chake ndikuti, ‘Mvereni;  
inenso ndikukuwuzani zimene ndikuzidziwa.’   
11 Ndadikira nthawi yonseyi,  
ndimamvetsera mwachidwi zimene mumayankhula,  
pamene mumafunafuna mawu oti muyankhule,   
12 ineyo ndinakumvetseranidi.  
Koma palibe ndi mmodzi yemwe wa inu amene anatsutsa Yobu;  
palibe aliyense wa inu amene anamuyankha mawu ake.   
13 Musanene kuti, ‘Ife tapeza nzeru;  
Mulungu ndiye amutsutse, osati munthu.’   
14 Koma Yobu sanayankhule motsutsana ndi ine,  
ndipo ine sindimuyankha monga mmene inu mwamuyankhira.   
   
 
15 “Iwo asokonezeka ndipo alibe choti ayankhulenso;  
mawu awathera.   
16 Kodi ine ndidikire chifukwa iwo sakuyankhula tsopano,  
pakuti angoyima phee wopanda yankho?   
17 Inenso ndiyankhulapo tsopano;  
nanenso ndinena zimene ndikudziwa.   
18 Pakuti ndili nawo mawu ambiri,  
ndipo mtima wanga ukundikakamiza;   
19 mʼkati mwanga ndili ngati botolo lodzaza ndi vinyo,  
ngati matumba a vinyo watsopano amene ali pafupi kuphulika.   
20 Ndiyenera kuyankhula kuti mtima utsike;  
ndiyenera kutsekula pakamwa panga ndi kuyankha.   
21 Sindidzakondera munthu wina aliyense,  
kapena kuyankhula zoshashalika,   
22 pakuti ndikanakhala wa luso loyankhula moshashalika,  
Mlengi wanga akanandilanga msanga.”