25
Mawu a Bilidadi 
 
1 Apo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,   
2 “Ulamuliro ndi kuopsa ndi za Mulungu,  
Iye amakhazikitsa bata mu ufumu wake kumwambako.   
3 Kodi magulu ake ankhondo nʼkuwerengeka?  
Kodi kuwala kwake sikuwalira ndani?   
4 Kodi munthu angakhale bwanji wolungama pamaso pa Mulungu?  
Kodi munthu wobadwa mwa mayi angakhale wangwiro?   
5 Ngati mwezi sutha kuwala kwenikweni,  
ndipo nyenyezi sizitha kuwala pamaso pake,   
6 nanji tsono munthu amene ali ngati mphutsi,  
mwana wa munthu amene ali ngati nyongolotsi!”