14
1 “Munthu wobadwa mwa amayi  
amakhala masiku owerengeka ndipo ndi odzaza ndi mavuto okhaokha.   
2 Amaphuka ngati duwa ndipo kenaka amafota;  
amathawa ngati mthunzi ndipo sakhalitsa.   
3 Kodi munthu wotereyo nʼkumuyangʼanitsitsa?  
Kodi mungamubweretse pamaso panu kuti mumuzenge mlandu?   
4 Ndani angatulutse chabwino mʼchoyipa?  
Palibe ndi mmodzi yemwe!   
5 Masiku a munthu ndi odziwikiratu;  
munakhazikitsa chiwerengero cha miyezi yake  
ndipo munamulembera malire amene sangathe kuwalumpha.   
6 Choncho Inu mumufulatire ndipo mumuleke apumule  
kufikira atakondwera nawo moyo ngati munthu waganyu.   
   
 
7 “Mtengo uli nacho chiyembekezo:  
ngati wadulidwa, udzaphukiranso  
ndipo nthambi zake sizidzaleka kuphukira.   
8 Mizu yake ingathe kukalamba mʼnthaka  
ndipo chitsa chake nʼkuwola pa dothi,   
9 koma pamene chinyontho chafika udzaphukira  
ndipo udzaphuka nthambi ngati mtengo wanthete.   
10 Koma munthu amafa nayikidwa mʼmanda,  
amapuma mpweya wotsiriza ndipo kutha kwake nʼkomweko.   
11 Monga madzi amaphwera mʼnyanja  
kapena monga mtsinje umaphwera nuwuma,   
12 momwemonso munthu amagona ndipo sadzukanso;  
mpaka zamlengalenga zidzathe, anthu sadzauka  
kapena kudzutsidwa ku tulo tawo.   
   
 
13 “Aa, Inu mukanangondibisa mʼmanda  
ndi kundiphimba kuti ndisaoneke mpaka mkwiyo wanu utapita!  
Achikhala munandiyikira nthawi,  
kuti pambuyo pake mundikumbukirenso.   
14 Munthu akafa, kodi adzakhalanso ndi moyo?  
Masiku anga onse a moyo wovutikawu  
ndidzadikira mpaka itafika nthawi yomasulidwa.   
15 Inu mudzandiyitane ndipo ndidzakuyankhani;  
inu mudzafunitsitsa kuona cholengedwa chimene munachipanga ndi manja anu.   
16 Ndithudi pamenepo mudzayangʼana mayendedwe anga  
koma simudzalondola tchimo langa.   
17 Zolakwa zanga zidzakulungidwa mʼthumba;  
inu mudzaphimba tchimo langa.   
   
 
18 “Koma monga phiri limakokolokera ndi kuswekasweka  
ndipo monga thanthwe limasunthira kuchoka pa malo ake,   
19 monganso madzi oyenda amaperesera miyala  
ndipo madzi othamanga amakokololera nthaka,  
momwemonso Inu mumawononga chiyembekezo cha munthu.   
20 Inu mumamugonjetsa kamodzinʼkamodzi ndipo munthuyo nʼkutheratu;  
Inu mumasintha maonekedwe a nkhope yake ndipo mumamutaya kutali.   
21 Ana ake akamalemekezedwa, iyeyo sazidziwa zimenezo;  
akamachititsidwa manyazi iye saziona zimenezo.   
22 Iye amangomva zowawa za mʼthupi lake  
ndipo amangodzilirira yekha mwini wakeyo.”