61
Uthenga Wabwino wa Yehova 
 
1 Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine,  
chifukwa Yehova wandidzoza  
kuti ndilalikire uthenga wabwino kwa anthu osauka.  
Wandituma kuti ndikatonthoze anthu osweka mtima,  
ndikalengeze kwa akapolo kuti alandire ufulu  
ndiponso kuti ndikamasule a mʼndende.   
2 Wandituma kuti ndikalengeze nthawi imene Yehova adzapulumutsa anthu ake;  
za tsiku limene Yehova adzalanga adani a anthu ake.  
Wandituma kuti ndikatonthoze olira.   
3 Wandituma kuti ndiwakonzere olira a ku Ziyoni,  
nkhata ya maluwa yokongola  
mʼmalo mwa phulusa,  
ndiwapatse mafuta achikondwerero  
mʼmalo mwa kulira.  
Ndiwapatse chovala cha matamando  
mʼmalo mwa mtima wopsinjika.  
Ndipo iwo adzatchedwa mitengo ya thundu yamphamvu yachilungamo,  
yoyidzala Yehova  
kuti Iye mwini apezemo ulemerero wake.   
   
 
4 Adzamanganso mabwinja akale a mzinda  
ndipo malo amene anawonongeka kalekale aja adzakonzanso.  
Adzakonzanso mizinda imene inapasuka,  
imene yakhala yowonongeka kwa nthawi yayitali kwambiri.   
5 Anthu achilendo adzakutumikirani; adzazidyetsa ziweto zanu;  
iwo adzagwira ntchito mʼminda yanu ya mpesa.   
6 Ndipo inu mudzatchedwa ansembe a Yehova,  
adzakutchulani kuti ndinu atumiki a Mulungu wathu.  
Mudzadyerera chuma cha mitundu ya anthu,  
ndipo mudzanyadira ulemu umene mwalandira.   
   
 
7 Chifukwa manyazi awo anali owirikiza;  
ndi kuti munalandira  
chitonzo ndi kutukwana,  
adzakondwera ndi cholowa chawo,  
tsono adzalandira cholowa chawo cha chigawo cha dziko mowirikiza,  
ndipo chimwemwe chamuyaya chidzakhala chawo.   
   
 
8 “Pakuti Ine Yehova, ndimakonda chilungamo;  
ndimadana ndi zakuba ndi zoyipa.  
Anthu anga ndidzawapatsa mphotho mokhulupirika  
ndikupangana nawo pangano losatha.   
9 Ana awo adzakhala odziwika pakati pa mitundu ya anthu  
ndipo adzukulu awo adzakhala otchuka pakati pa anthu a mitundu ina.  
Aliyense wowaona adzazindikira  
kuti ndi anthu amene Yehova wawadalitsa.”   
   
 
10 Ine ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Yehova;  
moyo wanga ukukondwera chifukwa cha Mulungu wanga.  
Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso,  
ndipo wandiveka mkanjo wachilungamo.  
Zili ngati mkwati wovala nkhata ya maluwa mʼkhosi mwake,  
ndiponso ngati mkwatibwi wovala mikanda yamtengowapatali.   
11 Monga momwe nthaka imameretsa mbewu  
ndiponso monga munda umakulitsa mbewu zimene anadzala,  
momwemonso Ambuye Yehova adzaonetsa chilungamo ndi matamando  
pamaso pa mitundu yonse ya anthu.