25
Nyimbo Yotamanda Yehova 
 
1 Yehova ndinu Mulungu wanga;  
ine ndidzakukwezani ndi kutamanda dzina lanu,  
pakuti mwachita zodabwitsa  
zimene munakonzekeratu kalekale  
mokhulupirika kwambiri.   
2 Inu mwasandutsa mzinda uja kukhala mulu wamiyala.  
Ndipo mzinda wamalinga wasanduka bwinja,  
linga la anthu achilendo lero si mzindanso  
ndipo sidzamangidwanso.   
3 Nʼchifukwa chake anthu amphamvu adzakulemekezani;  
mizinda ya mitundu ya anthu ankhanza idzakuopani.   
4 Inu mwakhala ngati populumukira pa anthu osauka,  
mwakhala ngati kobisalirako munthu wovutika pa nthawi ya masautso ake.  
Mwakhala ngati pobisalirapo  
pa nthawi ya mphepo yamkuntho ndi mthunzi pa nthawi ya dzuwa.  
Pakuti anthu ankhanza  
ali ngati mphepo yamkuntho yowomba pa khoma,   
5 ndiponso ngati kutentha mʼdziko lowuma.  
Inu mumaletsa phokoso la anthu achilendo.  
Monga momwe mthunzi wa mtambo umachepetsa kutentha,  
inu munaletsa nyimbo za anthu ankhanza.   
   
 
6 Pa phiri ili Yehova Wamphamvuzonse adzakonzera  
anthu a mitundu yonse madyerero a zakudya zokoma ndi vinyo wabwino.  
Phwando la nyama yonona  
ndi vinyo wabwino kwambiri.   
7 Iye adzachotsa kulira  
kumene kwaphimba anthu ngati nsalu.  
Adzachotsa chinsalu chimene chakuta mitundu yonse ya anthu.   
8 Yehova adzathetsa imfa mpaka muyaya,  
Ambuye Yehova adzapukuta misozi mʼmaso  
mwa munthu aliyense;  
adzachotsa manyazi a anthu ake  
pa dziko lonse lapansi,  
Yehova wayankhula.   
9 Tsiku limenelo iwo adzati,  
“Ndithudi, uyu ndiye Mulungu wathu;  
ife tinamudalira ndipo anatipulumutsa.  
Uyu ndiye Yehova, ife tinamudalira;  
tiyeni tikondwe ndi kusangalala chifukwa watipulumutsa.”   
   
 
10 Yehova adzateteza phiri limeneli ndi dzanja lake;  
ndipo Amowabu adzawapondereza pomwe alilipo,  
ngati mmene amapondera manyowa mʼdzenje.   
11 Amowabuwo adzatambasula manja awo mʼmenemo,  
ngati mmene amachitira munthu wosambira.  
Koma Mulungu adzathetsa kunyada kwawo  
ngakhale luso la manja awo.   
12 Iye adzagumula malinga awo ataliatali  
ndipo adzawagwetsa  
ndi kuwaponya pansi,  
pa fumbi penipeni.