21
Za Chilango cha Babuloni 
 
1 Uthenga wonena za chipululu cha mʼmbali mwa Nyanja.  
Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya adzabwera ngati kamvuluvulu amene akuwomba modutsa mʼmbali ya nyanja,  
kuchokera ku chipululu,  
dziko lochititsa mantha.   
   
 
2 Ine ndaona zinthu zoopsa mʼmasomphenya:  
Wonyenga akunyenga, wofunkha akufunkha komanso owononga akuwononga.  
Elamu, yambani nkhondo! Mediya, zingani mzinda!  
Ine ndidzathetsa mavuto onse amene anayambitsa Ababuloni.   
   
 
3 Chifukwa cha zimenezi thupi langa likunjenjemera ndi mantha,  
ndikumva ululu ngati wa mayi amene akubereka;  
ndikuvutika kwambiri ndi zimene ndikumva,  
ndathedwa nzeru ndi zimene ndikuziona.   
4 Mtima wanga ukugunda,  
ndipo ndikunjenjemera ndi mantha;  
chisisira chimene ndakhala ndikuchifuna  
chasanduka chinthu choopsa kwa ine.   
   
 
5 Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya akukonza matebulo,  
akuyala mphasa,  
akudya komanso kumwa!  
Mwadzidzidzi anamva mawu akuti, “Dzukani inu ankhondo,  
pakani mafuta zishango zanu!”   
6 Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi;  
“Pita, kayike mlonda  
kuti azinena zimene akuziona.   
7 Taonani, anthu akubwera ali pa akavalo  
ndipo akuyenda awiriawiri,  
okwera pa bulu  
kapena okwera pa ngamira,  
mlondayo akhale tcheru kwambiri.”   
8 Ndipo mlondayo anafuwula kuti,  
“Ambuye anga, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa nsanja yolondera;  
Usiku uliwonse ndimakhala pa malo anga olondera.   
9 Taonani, uyo munthu akubwera atakwera pa galeta  
ali ndi gulu la akavalo.  
Mmodzi wa iwo akuti,  
‘Babuloni wagwa, wagwa!  
Mafano onse a milungu yake  
agwa pansi ndipo aphwanyika!’ ”   
   
 
10 Inu anthu anga opunthidwa ndi kupetedwa ngati tirigu,  
ine ndikukuwuzani zimene ndamva  
ndikukuwuzani Uthenga wochokera kwa Yehova Wamphamvuzonse,  
Mulungu wa Israeli.   
Za Chilango cha Edomu 
 
11 Uthenga wonena za Duma:  
Munthu wina akundiyitana kuchokera ku Seiri kuti,  
“Iwe mlonda, usikuwu utha liti?  
Iwe mlonda, utha liti kodi usikuwu?”   
12 Mlonda akuyankha kuti,  
“Kukucha, koma kudanso.  
Ngati ukufuna kufunsa, funsa tsopano;  
ndipo ubwerenso udzafunse.”   
Za Chilango cha Arabiya 
 
13 Uthenga wonena za Arabiya:  
Inu anthu amalonda a ku Dedani,  
amene usiku mumagona mʼzithukuluzi za ku Arabiya,   
14 perekani madzi kwa anthu aludzu.  
Inu anthu a ku Tema  
perekani chakudya kwa anthu othawa nkhondo.   
15 Iwo akuthawa malupanga,  
lupanga losololedwa,  
akuthawa uta wokokakoka  
ndiponso nkhondo yoopsa.   
16 Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi: “Chaka chimodzi chisanathe, potsata mmene amawerengera munthu waganyu, ulemerero wonse wa Kedara udzatheratu.  
17 Mwa anthu okoka uta, ankhondo a ku Kedara opulumuka adzakhala owerengeka.” Wayankhula ndi Yehova Mulungu wa Israeli.