49
Yakobo Adalitsa Ana ake Aamuna
Pambuyo pake Yakobo anayitanitsa ana ake aamuna nati: Sonkhanani pamodzi kuti ndikuwuzeni zimene zidzakuchitikireni mʼmasiku a mʼtsogolo.
“Bwerani ndipo imvani mawu anga, inu ana a Yakobo;
mverani abambo anu Israeli.
 
“Rubeni, ndiwe woyamba kubadwa;
mphamvu yanga ndiponso chizindikiro choyamba cha mphamvu zanga,
wopambana pa ulemerero ndi mphamvu.
Wokokoma ngati madzi a chigumula, koma sudzakhalanso wopambana,
iwe unagona pa bedi la abambo ako,
ndithu unayipitsa bedi la mdzakazi wake.
 
“Simeoni ndi Levi ndi pachibale pawo,
anachitira nkhanza anthu amene anachita nawo pangano.
Iwe moyo wanga, usakhale nawo pa misonkhano yawo ya mseri,
kapena kugwirizana nawo mʼmabwalo awo,
pakuti anapha anthu mu mkwiyo wawo
ndipo anapundula ngʼombe zamphongo monga kunawakomera.
Matemberero awagwere chifukwa cha mkwiyo wawo woopsa chonchi
ndi ukali wawo wankhanza choterewu!
Ine ndidzawabalalitsa mʼdziko la Yakobo
ndi kuwamwaza iwo mʼdziko la Israeli.
 
“Yuda, ndiwe amene abale ako adzatamanda;
dzanja lako lidzagwira pa khosi pa adani ako;
abale ako adzakugwadira iwe.
Yuda ali ngati mwana wa mkango;
umabwerera ku malo ako ndi zofunkha, mwana wanga.
Monga mkango, amadziwongola ndi kugona pansi,
ndipo ngati mkango waukazi, ndani angalimbe mtima kumudzutsa?
10 Ndodo yaufumu sidzachoka mwa Yuda,
udzawupanirira ulamuliro motero kuti palibe amene adzawuchotse,
mpaka mwini wake weniweni atabwera
ndipo mitundu yonse ya anthu idzamumvera.
11 Ndiye amene amamangirira bulu wake wamkazi kumtengo wa mpesa,
ndi mwana wa bulu ku nthambi ya mpesa wabwino.
Ndi iye amene amachapa zovala zake mu vinyo;
ndi mkanjo wake mu vinyo wofiira ngati magazi.
12 Maso ake adzakhala akuda chifukwa cha vinyo,
mano ake woyera chifukwa cha mkaka.
 
13 “Zebuloni adzakhala mʼmphepete mwa nyanja;
adzakhala pa dooko la sitima zapamadzi;
malire ake adzafika ku Sidoni.
 
14 “Isakara ali ngati bulu wamphamvu
wogona pansi pakati pa makola.
15 Ataona ubwino wake wa pamalo pake popumira
ndi kukongola kwa dziko lake,
iye anaweramutsa msana kuti anyamule katundu wake
ndipo anasanduka wogwira ntchito ya ukapolo.
 
16 “Dani adzaweruza mwachilungamo anthu ake
monga limodzi mwa mafuko a anthu a mu Israeli.
17 Dani adzakhala ngati njoka ya mʼmphepete mwa msewu,
songo yokhala mʼnjira
imene imaluma chidendene cha kavalo
kuti wokwerapoyo agwe chagada.
 
18 “Ndikuyembekeza chipulumutso chanu Yehova.
 
19 “Gadi adzachitidwa chiwembu ndi gulu la amaliwongo,
koma iye adzawathamangitsa.
 
20 “Dziko la Aseri lidzabereka chakudya chokoma,
ndipo iye adzapereka chakudya kwa mafumu.
 
21 “Nafutali ali ngati mbawala yayikazi
yokhala ndi ana okongola kwambiri.
 
22 “Yosefe ali ngati mtengo wobereka zipatso,
mtengo wobereka zipatso pafupi ndi kasupe,
nthambi zake zimayanga pa chipupa cha mwala.
23 Alenje a uta anamuchita chiwembu mwankhanza;
anamuthamangitsa ndi mauta awo.
24 Koma uta wake sunagwedezeke,
ndi manja ake amphamvu aja analimbika,
chifukwa cha mphamvu za Mulungu Wamphamvu wa Yakobo,
chifukwa ali Mʼbusa ndi Thanthwe la Israeli.
25 Chifukwa cha Mulungu wa makolo ako amene amakuthandiza;
chifukwa cha Mulungu Wamphamvu, amene amakudalitsa
ndi mvula yochokera kumwamba,
ndi madzi otumphuka pansi pa nthaka,
ndipo amakudalitsa pokupatsa ana ambiri ndi ngʼombe zambiri.
26 Madalitso a kholo lako ndi amphamvu kuposa
madalitso a mapiri akale
oposa zabwino za ku zitunda zamgonagona.
Zonse izi zikhale pamutu pa Yosefe,
pa mphumi pa wopatulika uja amene anapatulidwa pakati pa abale ake.
 
27 “Benjamini ali ngati mʼmbulu wolusa;
umene mmawa umapha ndi kudya zofunkha,
ndipo madzulo umagawa zofunkhazo,”
28 Onse awa ndi mafuko khumi ndi awiri a Israeli, ndipo zimenezi ndi zomwe abambo awo ananena pamene anawadalitsa, kuwapatsa aliyense madalitso ake womuyenera iye.
Kumwalira kwa Yakobo
29 Kenaka Yakobo analamula ana ake nati: “Ine ndatsala pangʼono kufa. Tsono mukandiyike pamodzi ndi makolo anga mʼphanga la mʼmunda wa Efroni Mhiti. 30 Ili ndi phanga la mʼmunda wa Makipela, pafupi ndi Mamre mʼdziko la Kanaani. Abrahamu anagula phangalo pamodzi ndi munda womwe kwa Efroni Mhiti kuti pakhale manda. 31 Kumeneko kunayikidwa Abrahamu ndi mkazi wake Sara, Isake ndi mkazi wake Rebeka ndipo ndinayikakonso Leya. 32 Munda ndi manda amene ali mʼmenemo zinagulidwa kwa Ahiti.”
33 Yakobo atamaliza kupereka malangizo kwa ana ake, anabwezera miyendo yake pa bedi, namwalira ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake.