34
Dina ndi Sekemu
Tsopano Dina, mwana amene Leya anaberekera Yakobo, anapita kukacheza ndi akazi ena a mʼdzikolo. Pamene Sekemu mwana wa Hamori Mhivi, mfumu ya deralo, anamuona, anamugwirira. Koma Sekemu anamukondadi namwali uja, Dina, mwana wa Yakobo motero kuti anamuyankhula mawu womutonthoza. Choncho Sekemu anati kwa abambo ake Hamori, “Mundipezere mtsikana uyu kuti akhale mkazi wanga.”
Yakobo anamva kuti mwana wake Dina wagwiriridwa, koma sanachitepo kanthu msanga kudikira mpaka ana ake amuna omwe anali ku busa atabwerako.
Kenaka Hamori, abambo a Sekemu, anapita kukakambirana ndi Yakobo. Pa nthawi iyi nʼkuti ana a Yakobo atabwererako ku busa kuja. Iwo atangomva zimene zinachitika, anawawidwa mtima. Iwo anapsa mtima kwambiri kuti Sekemu nʼkuchita chonyansa choterechi mu dziko la Israeli, kumugwirira Dina, mwana wa Yakobo.
Koma Hamori anawawuza kuti, “Mwana wanga Sekemu wamukonda kwambiri mwana wanu. Chonde muloleni kuti akhale mkazi wake. Tiyeni tichite mgwirizano wa ukwati kuti ife tidzikwatira ana anu ndi inu mudzikwatira ana athu. 10 Khazikikani pakati pathu. Mukhoza kupeza malo wokhala kulikonse kumene mufuna. Mukhozanso kuchita malonda momasuka ndi kupeza chuma.”
11 Pamenepo Sekemu anati kwa abambo ndi alongo ake a Dina, “Inu mundikomere mtima, ndipo ndidzakupatsani chilichonse munganene. 12 Tchulani mtengo wamalowolo umene ndiyenera kupereka, ndipo ndipereka. Ndidzakupatsani chilichonse chimene mukufuna malingana inu mukandipatsa namwaliyu kuti ndimukwatire.”
13 Ana a Yakobo anayankha Sekemu ndi abambo ake, Hamori mwachinyengo chifukwa mlongo wawo, Dina anali atayipitsidwa. 14 Iwo anati, “Sitingachite zimenezo, kupereka mlongo wathu kwa munthu wosachita mdulidwe. Chimenecho ndi chinthu cha manyazi kwa ife. 15 Tikuvomerani pokhapokha mutakhala ngati ife, mutachita mdulidwe ana anu onse aamuna. 16 Kenaka tidzakulolani kuti mukwatire ana athu, ifenso tizikwatira ana anu. Choncho tidzakhala pakati panu ndipo tidzakhala anthu amodzi. 17 Koma ngati simuvomereza kuchita mdulidwe titenga mlongo wathu ndi kupita.”
18 Mawu amenewa anakondweretsa Hamori ndi mwana wake Sekemu. 19 Mnyamata uja amene anali wolemekezeka kwambiri pa banja lake lonse, sanachedwe kuchita mdulidwe popeza anamukonda kwambiri mwana wa Yakobo. 20 Choncho Hamori ndi mwana wake Sekemu anapita ku chipata cha mzinda wawo kukayankhula ndi anthu a mu mzindawo. 21 Iwo anati, “Anthu awa ndi a mtendere. Aloleni kuti akhale mʼdziko mwathu muno nachitamo malonda. Dzikoli lili ndi malo ambiri woti iwo nʼkukhalamo. Tingathe kukwatira ana awo aakazi ndipo angathe kukwatira ana athu aakazi. 22 Komatu anthuwa adzavomereza kukhala amodzi a ife pokhapokha ngati amuna onse pakati pathu atachita mdulidwe monga alili iwo. 23 Tikatero, ndiye kuti ziweto zawo zonsezi, katundu wawo yenseyu ndi ziweto zawo zina zonsezi zidzakhala zathu. Choncho tiyeni tiwavomereze ndipo adzakhazikika pakati pathu.”
24 Amuna onse amene anatuluka ku chipata cha mzinda anavomerezana ndi Hamori ndi mwana wake Sekemu, ndipo aliyense wamwamuna mu mzindamo anachita mdulidwe.
25 Patapita masiku atatu, amuna onse akumvabe ululu wa kuchita mdulidwe uja, ana awiri a Yakobo, Simeoni ndi Levi, alongo ake a Dina, anatenga malupanga ndi kulowa mu mzindawo mwakachetechete napha amuna onse. 26 Anapha Hamori ndi Sekemu. Anakatenga Dina ku nyumba kwa Sekemu nanyamuka. 27 Ana a Yakobo anafika kwa anthu ophedwawo ndi kututa katundu mu mzindawo chifukwa anagwiririra mlongo wawo. 28 Analanda nkhosa zawo, ngʼombe zawo, abulu awo ndi china chilichonse chawo mu mzindamo pamodzi ndi za ku minda. 29 Anawatengera chuma chawo chonse, akazi ndi ana awo, pamodzi ndi zonse zimene zinapezeka mʼnyumba zawo. Zonsezi zinayesedwa ngati zolandidwa ku nkhondo.
30 Pamenepo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, “Mwandiputira mavuto, ndi kundiyipitsira dzina pakati pa anthu a mʼdziko lino, Akanaani ndi Aperezi. Ife ndife owerengeka, ndipo atati aphatikizane kudzandithira nkhondo, ndiye kuti ine ndi banja langa tidzawonongeka.”
31 Koma iwo anayankha kuti, “Pepani, nanga achite kumusandutsa mlongo wathu ngati mkazi wachiwerewere?”