29
Mwambo Wopatula Ansembe
1 “Pofuna kumupatula Aaroni ndi ana ake kuti akhale ansembe onditumikira Ine, uchite izi: Utenge ngʼombe yayingʼono yayimuna ndi nkhosa ziwiri zazimuna zopanda chilema.
2 Utengenso buledi wopanda yisiti, makeke wopanda yisiti wopakidwa mafuta. Zonsezi uzipange ndi ufa wosalala wa tirigu.
3 Uziyike mʼdengu ndipo ubwere nazo kwa Ine pamodzi ndi ngʼombe yayimuna ija ndi nkhosa ziwiri zazimuna zija.
4 Kenaka ubwere naye Aaroni ndi ana ake pa khomo la tenti ya msonkhano ndipo uwasambitse ndi madzi.
5 Tenga zovala ndipo umuveke Aaroni mwinjiro, mkanjo wa efodi, efodiyo ndi chovala chapachifuwa. Umumange mʼchiwuno lamba wa efodi wolukidwa mwaluso uja.
6 Umuveke nduwira kumutu, ndiponso uyike chizindikiro chopatulika chija pa nduwirayo.
7 Utenge mafuta wodzozera ndipo uwatsanulire pamutu pake kumudzoza.
8 Ubwere ndi ana ake aamuna ndipo uwavekenso minjiro
9 ndi nduwira. Kenaka umange malamba Aaroniyo pamodzi ndi ana ake ndi kuwaveka nduwira. Motero unsembe udzakhala wawo malingana ndi lamulo ili losatha.
“Umu ndi mmene udzadzozere Aaroni ndi ana ake aamuna.
10 “Ubwere ndi ngʼombe yayimuna pa khomo la tenti ya msonkhano ndipo Aaroni ndi ana ake asanjike manja awo pamutu pake.
11 Uphe ngʼombeyo pamaso pa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano.
12 Utenge magazi ena angʼombeyo ndi kupaka ndi chala chako pa nyanga zaguwa lansembe ndipo magazi otsalawo uwakhutulire pa tsinde laguwalo.
13 Kenaka utenge mafuta onse okuta matumbo, mafuta ophimba chiwindi ndiponso impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta ake. Zonsezi uzitenthe pa guwapo.
14 Koma nyama yangʼombeyo, chikopa chake ndi matumbo ake uziwotche kunja kwa msasa. Iyi ndi nsembe yopepesera machimo.
15 “Utenge nkhosa yayimuna imodzi ndipo Aaroni ndi ana ake aamuna asanjike manja awo pamutu pake.
16 Uyiphe ndipo utenge magazi ake ndi kuwaza mbali zonse zaguwalo.
17 Uyidule nkhosayo nthulinthuli, kutsuka matumbo ake ndi miyendo yake. Ukatero, pamodzi ndi mutu wake, uziyike pamwamba pa nthulizo.
18 Ndipo uwotche nkhosa yonseyo pa guwa lansembe. Iyi ndi nsembe yopsereza ya kwa Yehova. Ili ndi fungo lokoma, loperekedwa pa moto kwa Yehova.
19 “Utenge nkhosa yayimuna ina ndipo Aaroni ndi ana ake aamuna asanjike manja awo pamutu pake.
20 Uyiphe ndipo utenge magazi ake ena ndi kupaka ndewere za makutu a kudzanja lamanja la Aaroni ndi ana ake aamuna. Upakenso pa zala zawo zazikulu za kudzanja lawo lamanja, ndi zala zazikulu za kuphazi lakudzanja lawo lamanja. Kenaka uwaze magazi otsalawo mbali zonse za guwalo.
21 Ndipo utenge magazi ena amene ali pa guwa lansembe komanso pa mafuta ena odzozera ndipo uwawaze pa Aaroni ndi zovala zake ndi ana ake ndi zovala zawo. Ndiye kuti iyeyo ndi ana ake aamuna adzakhala opatulika pamodzi ndi zovala zawo.
22 “Pa nkhosa yayimuna ija utengepo mafuta ake, mafuta a ku mchira wake, mafuta okuta matumbo, mafuta okuta chiwindi, impsyo zonse ziwiri ndi mafuta ake, ndiponso ntchafu yakumanja. Iyi ndi nkhosa ya mwambo wodzoza.
23 Utengenso mʼdengu la buledi wopanda yisiti limene lili pamaso pa Yehova, buledi mmodzi, buledi wokhala ndi mafuta a olivi, ndi buledi wopyapyala mmodzi.
24 Izi zonse uzipereke mʼmanja mwa Aaroni ndi ana ake, ndipo iwo aziweyule pamaso pa Yehova kuti zikhale nsembe yoweyula.
25 Kenaka uzitenge mʼmanja mwawo ndipo uzipsereze pa guwa lansembe, pamwamba penipeni pamodzi ndi nsembe yopsereza kuti ipereke fungo lokoma kwa Yehova. Ichi ndiye chopereka chachakudya kwa Yehova.
26 Kenaka utenge chidale cha nkhosa yayimuna imene inaperekedwa pamwambo wodzoza Aaroni, uchiweyule kuti chikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova ndipo chidzakhala gawo lako.
27 “Uzipatule ziwalo zonse za nkhosa ya pa mwambo wodzoza Aaroni ndi ana ake. Chidale chimene unaweyula chija ndiponso ntchafu imene inaperekedwa ija.
28 Nsembe izi ndi zimene Aisraeli azipereka kwa Aaroni ndi ana ake mwa zonse zimene azipereka nthawi zonse. Mwa zopereka za mtendere zimene ana a Aisraeli adzapereka kwa Yehova, zimenezi zikhale gawo lawo.
29 “Zovala zopatulika za Aaroni zidzakhala za ana ake aamuna iye atafa kuti adzavale podzozedwa ndi polandira udindo wawo.
30 Mwana amene adzalowa mʼmalo mwake monga wansembe pamene adzabwerera kudzalowa mu tenti ya msonkhano kudzatumikira ku malo wopatulika, adzavala zovala zimenezi masiku asanu ndi awiri.
31 “Utenge nkhosa yayimuna ya pamwambo wodzoza ansembe ndipo uyiphike pamalo opatulika.
32 Aaroni ndi ana ake adye nyama ya nkhosa yayimunayi pamodzi ndi buledi amene ali mʼdengu pa khomo la tenti ya msonkhano.
33 Adye zonse zimene anazipereka kwa Yehova pamwambo wopepesera machimo powadzoza ndi kuwapatula. Munthu wamba asadye chifukwa ndi zopatulika.
34 Ndipo ngati nyama ina ya nkhosa ya pamwambo wodzoza ansembe kapena buledi zatsala mpaka mmawa, muziwotche, asazidye chifukwa ndi zopatulika.
35 “Uchitire Aaroni ndi ana ake aamuna zonse zimene ndakulamulazi. Uchite mwambo wowapatula kukhala ansembe masiku asanu ndi awiri.
36 Tsiku lililonse uzipereka ngʼombe yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo kuti machimowo akhululukidwe. Ndiponso upatule guwalo popereka nsembe yopepesera ndi kulidzoza mafuta kuti likhale lopatulika.
37 Pa masiku asanu ndi awiri uzipereka pa guwapo nsembe zoyeretsera guwalo, ukatero ndiye kuti uzilipatula. Ndipo guwa lansembelo lidzakhala loyera kwambiri, ndipo chilichonse chimene chidzakhudza guwalo chidzayeretsedwa.
38 “Tsiku ndi tsiku pa guwa lansembe uzipereka izi: Ana ankhosa a chaka chimodzi awiri.
39 Mmawa muzipereka mwana wankhosa mmodzi ndipo winayo madzulo.
40 Pamodzi ndi mwana wankhosa woyambayo, muzipereka kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi lita imodzi ya mafuta a olivi pamodzi ndi lita imodzi ya vinyo ngati chopereka chachakumwa.
41 Upereke mwana wankhosa winayo madzulo pamodzi ndi chopereka chachakudya monga poyamba paja ndi chopereka chachakumwa monga mmawa kuti ikhale fungo lokoma la chopereka chachakudya kwa Yehova.
42 “Zopereka zopsereza zimenezi ziziperekedwa nthawi zonse, pa mibado yonse. Muzidzazipereka pamaso pa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano. Pa guwa lansembe, Yehova adzakumana nanu ndi kuyankhula nanu.
43 Pameneponso Ine ndidzakumana ndi Aisraeli, ndipo guwalo lidzakhala lopatulika chifukwa cha ulemerero wanga.
44 “Tsono Ine ndidzapatula tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe. Ndidzapatulanso Aaroni pamodzi ndi ana ake kuti akhale ansembe anga onditumikira.
45 Ndidzakhala pakati pa Aisraeli ndikukhala Mulungu wawo.
46 Adzadziwa kuti ine ndine Mulungu wawo amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto kuti ndikhale pakati pawo. Ine ndine Yehova, Mulungu wawo.”